Yoh. 2

2
Ukwati wa ku Kana
1Patapita masiku aŵiri, kunali ukwati ku mudzi wa Kana m'dera la Galileya. Amai ake a Yesu anali komweko. 2Yesu nayenso pamodzi ndi ophunzira ake adaaitanidwa kuukwatiko. 3Pamene vinyo adatha, amai ake a Yesu adamuuza kuti, “Waŵathera vinyo.” 4Yesu adayankha kuti, “Mai, kodi mukuti nditani? Nthaŵi yangatu siinafike.” 5Apo amai ake adauza anyamata amene ankatumikira kuti, “Chilichonse chimene akuuzeni, muchite.”
6Pamenepo panali mbiya zamwala zisanu ndi imodzi, zimene adaaziikapo chifukwa cha mwambo wa kudziyeretsa#2.6: Mwambo wa kudziyeretsa: Onani pa Mk. 7.3-5. wa Ayuda. M'mbiya iliyonse munkaloŵa madzi okwanira malita zana limodzi kapena kupitirirapo. 7Tsono Yesu adauza anyamata aja kuti, “Dzazani mbiyazi ndi madzi.” Ndipo adazidzaza mpaka m'milomo. 8Pambuyo pake adaŵauza kuti, “Tsopano tungani, kaperekeni kwa mkulu wa phwando,” Iwowo adakaperekadi. 9Mkulu wa phwandoyo adalaŵa madzi osanduka vinyowo osadziŵa kumene achokera. (Koma anyamata aja amene adaatunga madziwo ankadziŵa.) Tsono mkulu wa phwandoyo adaitana mkwati, 10namuuza kuti, “Anzanu amapereka vinyo wabwino kwambiri poyamba, kenaka anthu atakhuta, amaŵapatsa vinyo wokoma pang'ono. Koma inu mwasunga vinyo wabwino kwambiri kufikira tsopano.”
11Yesu adaonetsa chizindikiro chake choyambachi m'mudzi wa Kana m'dera la Galileya. Pamenepo adaonetsa ulemerero wake, ndipo ophunzira ake adamkhulupirira.
12 # Mt. 4.13 Pambuyo pake Yesu adapita ku Kapernao, pamodzi ndi amai ake ndi abale ake ndi ophunzira ake, ndipo adakhala kumeneko masiku oŵerengeka.
Yesu ayeretsa Nyumba ya Mulungu
(Mt. 21.12-13; Mk. 11.15-18; Lk. 19.45-46)
13 # Eks. 12.1-27 Itayandikira nthaŵi ya Paska, chikondwerero cha Ayuda, Yesu adanyamuka kupita ku Yerusalemu. 14Kumeneko adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu napezamo anthu akugulitsa ng'ombe, nkhosa ndi nkhunda. Munalinso anthu osinthitsa ndalama.#2.14: osinthitsa ndalama: Pa bwalo lina la Nyumba ya Mulungu ankagulitsa zoŵeta zoti anthu apereke nsembe. Ndipo ankasinthitsa ndalama zachiroma ndi ndalama zachiyuda, popeza kuti ku Nyumba ya Mulungu sankalola zopereka za ndalama zachiroma ai. 15Apo Yesu adapanga mkwapulo wazingwe nayamba kuŵatulutsira onse kunja, pamodzi ndi nkhosa ndi ng'ombe zao zomwe. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama aja, naŵamwazira ndalama zao. 16Ndipo adalamula ogulitsa nkhunda aja kuti, “Izi zitulutseni muno. Nyumba ya Atate anga musaisandutse nyumba yochitiramo malonda.” 17#Mas. 69.9Ophunzira ake adakumbukira Malembo aja akuti, “Changu chomwe ndimachitira nyumba yanu chidzandiphetsa.”
18Pamenepo akuluakulu a Ayuda adamufunsa kuti, “Kodi mungatiwonetse chizindikiro chotani chakuti muli ndi ulamuliro wochitira zimenezi?” 19#Mt. 26.61; 27.40; Mk. 14.58; 15.29Yesu adaŵayankha kuti, “Gwetsani nyumba ya Mulungu ino, Ine ndidzaimanganso masiku atatu.” 20Apo iwo adati, “Nyumba ya Mulunguyi idatenga zaka 46 kuti aimange, tsono Inu nkuimanga masiku atatu chabe?” 21Koma Yesu ankanena za thupi lake mophiphiritsa, pamene adaatchula Nyumba ya Mulungu. 22Iye atauka kwa akufa, ophunzira ake adadzakumbukira kuti adaanena zimenezi, nakhulupirira Malembo ndiponso mau amene Yesu adaanenawo.
Yesu amadziŵa anthu onse
23Pamene Yesu anali m'Yerusalemu pa chikondwerero cha Paska, anthu ambiri adayamba kuika chikhulupiriro chao pa Iye, poona zozizwitsa zimene ankachita. 24Koma Yesu sadaikepo chikhulupiriro pa iwowo, popeza kuti Iye ankaŵadziŵa anthu onse. 25Sankalira kuti wina achite chomuuza za munthu aliyense. Pakuti mwiniwakeyo ankadziŵa za m'mitima mwa anthu.

S'ha seleccionat:

Yoh. 2: BLY-DC

Subratllat

Comparteix

Copia

None

Vols que els teus subratllats es desin a tots els teus dispositius? Registra't o inicia sessió