GENESIS 27:39-40
GENESIS 27:39-40 BLPB2014
Ndipo Isaki atate wake anayankha nati kwa iye, Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi, pa mame a kumwamba akudzera komwe. Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako.