YOHANE 10

10
Za Mbusa Wabwino
1Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m'khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda. 2Koma iye wakulowera pakhomo, ndiye mbusa wa nkhosa. 3Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja. 4Pamene adatulutsa zonse nkhosa zimtsata iye; chifukwa zidziwa mau ake. 5Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthawa; chifukwa sizidziwa mau a alendo. 6Fanizo ili Yesu ananena kwa iwo; koma sanazindikira zimene Yesu analikulankhula nao.
7Chifukwa chake Yesu ananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa. 8Onse amene anadza m'tsogolo mwa Ine ali akuba, ndi olanda: koma nkhosa sizinamva iwo. 9#Yoh. 14.6; Aef. 2.18Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa. 10Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka. 11#Mas. 23; Yes. 40.11; Aheb. 13.20Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa. 12#Zek. 11.16-17Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa sizili zake za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa; 13chifukwa ali wolipidwa, ndipo sasamala nkhosa. 14#2Tim. 2.19Ine ndiye Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira Ine, 15#Mat. 11.27; Yoh. 15.13monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa. 16#Yes. 56.8; Aef. 2.14Ndipo nkhosa zina ndili nazo, zimene sizili za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi. 17Chifukwa cha ichi Atate andikonda Ine, chifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso. 18#Yoh. 2.19Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga.
19Panakhalanso kutsutsana pakati pa Ayuda chifukwa cha mau awa. 20#Yoh. 7.20Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi chiwanda, nachita misala; mukumva Iye bwanji? 21Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa chiwanda. Kodi chiwanda chikhoza kumtsegulira maso wosaona?
Yesu adziwulula ali Mwana wa Mulungu
22Koma kunali phwando la kukonzetsanso m'Yerusalemu; nyengoyo ndi yachisanu. 23Ndipo Yesu analikuyendayenda m'Kachisi m'khonde la Solomoni. 24Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiuzeni momveka. 25#Yoh. 5.36Yesu anayankha iwo, Ndakuuzani, ndipo simukhulupirira. Ntchitozi ndidzichita Ine m'dzina la Atate wanga, zimenezi zindichitira umboni. 26#Yoh. 8.47Koma inu simukhulupirira, chifukwa simuli a mwa nkhosa zanga. 27#Yoh. 8.4, 14Nkhosa zanga zimva mau anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine. 28#Yoh. 6.37; 12; 17.11; 18.9Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa. 29Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina ngathe kuzikwatula m'dzanja la Atate. 30#Yoh. 17.22Ine ndi Atate ndife amodzi. 31#Yoh. 8.59Ayuda anatolanso miyala kuti amponye Iye. 32Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala? 33#Yoh. 5.18Ayuda anamyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu. 34#Mas. 82.6Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'chilamulo chanu, Ndinati Ine, Muli milungu? 35Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka), 36#Yoh. 8.42kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu? 37Ngati sindichita ntchito za Atate wanga, musakhulupirira Ine. 38#Yoh. 5.36; 10.25; 14.10-11Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi Ine mwa Atate. 39Anafunanso kumgwira Iye; ndipo anapulumuka m'dzanja lao.
40Ndipo anachoka kunkanso tsidya lija la Yordani, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko. 41#Yoh. 3.27-30Ndipo ambiri anadza kwa Iye; nanena kuti, Sanachita chizindikiro Yohane; koma zinthu zilizonse Yohane ananena za Iye zinali zoona. 42#Yoh. 8.30; 11.45Ndipo ambiri anakhulupirira Iye komweko.

נבחרו כעת:

YOHANE 10: BLPB2014

הדגשה

שתף

העתק

None

רוצים לשמור את ההדגשות שלכם בכל המכשירים שלכם? הירשמו או היכנסו