LUKA 11

11
Pemphero la Ambuye
(Mat. 6.9-13)
1Ndipo kunali, pakukhala Iye pamalo pena ndi kupemphera, m'mene analeka, wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake. 2Ndipo anati kwa iwo, M'mene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwa; Ufumu wanu udze; 3tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku. 4Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.
Fanizo la bwenzi laliuma
5Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu; 6popeza wandidzera ndipo ndilibe chompatsa; 7ndipo iyeyu wa m'katimo poyankha akati, Usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindikhoza kuuka ndi kukupatsa? 8#Luk. 18.1-6Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye zilizonse azisowa. 9#Mat. 7.7; Yoh. 15.7; Yak. 1.6; 1Yoh. 3.22Ndipo Ine ndinena ndi inu, Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani. 10Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofuna apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira. 11#Mat. 7.9-12Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba? 12#Mat. 7.9-12Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira? 13#Mat. 7.9-12Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?
Za Yesu ndi Belezebulu
(Mat. 12.22-32; Mrk. 3.22-30)
14Ndipo analikutulutsa chiwanda chosalankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa. 15Koma ena mwa iwo anati, Ndi Belezebulu mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda. 16Koma ena anamuyesa, nafuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba. 17#Yoh. 2.25; Mrk. 3.24Koma Iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika m'kati mwake upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwake igwa. 18Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wake? Popeza munena kuti nditulutsa ziwanda ndi Belezebulu. 19Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Belezebulu, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala oweruza anu. 20Koma ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu. 21#Mrk. 3.27Pamene paliponse mwini mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake zili mumtendere; 22koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamlaka, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake. 23Iye wosavomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza. 24#Mat. 12.43-45Pamene paliponse mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinatulukako; 25#Mat. 12.43-45ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka. 26#Mrk. 3.27; Yoh. 5.14; Aheb. 6.4; 2Pet. 2.20Pomwepo upita nutenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe otsiriza a munthu uyu aipa koposa oyambawo.
27Ndipo kunali, pakunena izi Iye, mkazi wina mwa khamu la anthu anakweza mau, nati kwa Iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene munayamwa. 28#Mat. 7.21; Yak. 1.25Koma Iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga.
Chizindikiro cha Yona
(Mat. 12.38-42)
29Ndipo pakusonkhana pamodzi makamu a anthu, anayamba kunena, Mbadwo uno ndi mbadwo woipa; ufuna chizindikiro, ndipo chizindikiro sichidzapatsidwa kwa uwu koma chizindikiro cha Yona. 30#Yon. 1.17; 2.10Pakuti monga ngati Yona anali chizindikiro kwa Aninive, chotero adzakhalanso Mwana wa Munthu kwa mbadwo uno. 31#1Maf. 10.1Mfumu yaikazi ya kumwera idzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza kuchokera kumalekezero a dziko kudzamva nzeru za Solomoni; ndipo onani, woposa Solomoni ali pano. 32#Yon. 3.5Amuna a ku Ninive adzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti iwo analapa pa kulalikira kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano.
Za nyali ya thupi
(Mat. 5.15-16)
33Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika. 34#Mat. 6.22Nyali ya thupi ndiyo diso lako; pamene paliponse diso lako lili langwiro thupi lako lonse liunikidwanso monsemo; koma likakhala loipa, thupi lako lomwe lili la mdima wokhawokha. 35Potero yang'anira kuunika kuli mwa iwe kungakhale mdima. 36Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lake lamdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwake ikuunikira iwe.
Yesu adzudzula Alembi ndi Afarisi
(Mat. 23.1-39)
37Ndipo pakulankhula Iye, anamuitana Mfarisi kuti adye naye; ndipo analowa naseama kudya. 38#Mrk. 7.3Ndipo anazizwa Mfarisiyo, pakuona kuti anayamba chakudya asanasambe. 39#Mat. 23.25; Tit. 1.15Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'kati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa. 40Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m'kati mwake? 41Koma patsani mphatso yachifundo za m'katimo; ndipo onani, zonse zili zoyera kwa inu.
42 # Mat. 23.23 Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo. 43#Mat. 23.6Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando yaulemu m'masunagoge, ndi kupatsidwa moni m'misika. 44#Mat. 23.27Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.
45Ndipo mmodzi wa achilamulo anayankha, nanena kwa Iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso. 46#Mat. 23.4Ndipo anati, Tsoka inunso, achilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi. 47#Mat. 23.29Tsoka inu! Chifukwa mumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha. 48Chomwecho muli mboni, ndipo muvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda. 49#Mat. 23.34Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza; 50kuti mwazi wa aneneri onse, wakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno; 51#Gen. 4.8; 1Mbi. 24.20-21kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno. 52#Mat. 23.13Tsoka inu, achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa. 53Ndipo pamene Iye anatuluka m'menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza Iye kolimba, ndi kumtompha Iye ndi zinthu zambiri; 54#Mrk. 12.13namlindira akakole kanthu kotuluka m'kamwa mwake.

נבחרו כעת:

LUKA 11: BLPB2014

הדגשה

שתף

העתק

None

רוצים לשמור את ההדגשות שלכם בכל המכשירים שלכם? הירשמו או היכנסו