LUKA 7

7
Kenturiyo wa ku Kapernao
(Mat. 8.5-13)
1Pamene Yesu adamaliza mau ake onse m'makutu a anthu, analowa m'Kapernao.
2Ndipo kapolo wa kenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kutsirizika. 3Ndipo pamene iye anamva za Yesu, anatuma kwa Iye akulu a Ayuda, namfunsa Iye kuti adze kupulumutsa kapolo wake. 4Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha Iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi; 5pakuti akonda mtundu wathu, ndipo anatimangira ife sunagoge. 6Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi panyumba yake, kenturiyo anatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa chindwi langa; 7chifukwa chake ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu: koma nenani mau, ndipo mnyamata wanga adzachiritsidwa. 8Pakuti inenso ndili munthu wakumvera akulu anga, ndili nao asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tachita ichi, nachita. 9Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeza, ngakhale mwa Israele, chikhulupiriro chachikulu chotere. 10Ndipo pakubwera kunyumba otumidwawo, anapeza kapoloyo wachira ndithu.
Aukitsa mnyamata ku Nayini
11Ndipo kunali, katapita kamphindi, Iye anapita kumudzi, dzina lake Naini; ndipo ophunzira ake ndi mpingo waukulu wa anthu anapita naye. 12Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mudziwo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri akumudzi anali pamodzi naye. 13Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire. 14#Luk. 8.54; Mac. 9.40; Aro. 4.17Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka. 15Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake. 16#Luk. 1.68; 24.19; Yoh. 6.14Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake. 17Ndipo mbiri yake imeneyo inabuka ku Yudeya lonse, ndi ku dziko lonse loyandikira.
Amithenga a Yohane Mbatizi
(Mat. 11.1-19)
18Ndipo ophunzira a Yohane anamuuza iye zonsezi. 19Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina? 20Ndipo pakufika kwa Iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina? 21Nthawi yomweyo Iye anachiritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zovuta, ndi ziwanda; napenyetsanso anthu akhungu ambiri. 22#Yes. 35.5; Mat. 11.4-5; Luk. 4.18Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino. 23Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.
24 # Mat. 11.7 Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? 25Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zofewa kodi? Onani, iwo akuvala zolemera, ndi akukhala odyerera, ali m'nyumba za mafumu. 26Koma munatuluka kukaona chiyani? Mneneri kodi? Etu, ndinena kwa inu, ndipo wakuposa mneneri. 27#Mala. 3.1Uyu ndi iye amene kunalembedwa za iye,
Ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere,
amene adzakukonzera njira yako pamaso pako.
28Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane; koma iye amene ali wamng'ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye. 29#Mat. 3.5-6Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane. 30#Mac. 20.27Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye. 31#Mat. 11.16Ndipo, ndidzafanizira ndi chiyani anthu a mbadwo uno? Ndipo afanana ndi chiyani? 32Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzake, ndi kunena, Ife tinakulizirani chitoliro, ndipo inu simunavina ai; tinabuma maliro, ndimo simunalira ai. 33#Mat. 3.4Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo munena, Ali ndi chiwanda. 34Mwana wa Munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa! 35#Mat. 11.19Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ake onse.
Mkazi adzoza mapazi a Yesu
36Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana Iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m'nyumba ya Mfarisi, naseama pachakudya. 37Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene anali m'mudzimo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pachakudya m'nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino, 38naimirira kumbuyo, pa mapazi ake, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsompsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino. 39#Luk. 15.2Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa. 40Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndili ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anavomera, Mphunzitsi, nenani. 41Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ake a marupiya mazana asanu, koma mnzake makumi asanu. 42Popeza analibe chobwezera iwo, anawakhululukira onse awiri. Chotero, ndani wa iwo adzaposa kumkonda? 43Simoni anayankha, nati, Ndiyesa kuti, iye amene anamkhululukira zoposa. 44Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatsa madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake. 45Sunandipatsa mpsompsono wa chibwenzi; koma uyu sanaleke kupsompsonetsa mapazi anga, chilowere muno Ine. 46#Mas. 23.5Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino. 47#1Tim. 1.14Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang'ono, iye akonda pang'ono. 48#Mat. 9.2Ndipo anati kwa mkazi, Machimo ako akhululukidwa.
49 # Mat. 9.3 Ndipo iwo akuseama naye pachakudya anayamba kunena mwa okha, Uyu ndani amene akhululukiranso machimo? 50#Mat. 9.22Ndipo Iye anati kwa mkaziyo, Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

נבחרו כעת:

LUKA 7: BLPB2014

הדגשה

שתף

העתק

None

רוצים לשמור את ההדגשות שלכם בכל המכשירים שלכם? הירשמו או היכנסו