1
GENESIS 22:14
Buku Lopatulika
Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka.
Kokisana
Luka GENESIS 22:14
2
GENESIS 22:2
Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isaki, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.
Luka GENESIS 22:2
3
GENESIS 22:12
Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.
Luka GENESIS 22:12
4
GENESIS 22:8
Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwanawankhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri.
Luka GENESIS 22:8
5
GENESIS 22:17-18
kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mau anga.
Luka GENESIS 22:17-18
6
GENESIS 22:1
Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano.
Luka GENESIS 22:1
7
GENESIS 22:11
Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano.
Luka GENESIS 22:11
8
GENESIS 22:15-16
Ndipo mthenga wa Yehova anamuitana Abrahamu ndi mau odzera kumwamba kachiwiri, nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikanize mwana wako, mwana wako yekha
Luka GENESIS 22:15-16
9
GENESIS 22:9
Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isaki mwana wake, namuika iye paguwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.
Luka GENESIS 22:9
Ndako
Biblia
Bibongiseli
Bavideo