YOHANE 19
19
1 #
Mat. 20.19; 27.26 Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula. 2#Mat. 27.29Ndipo asilikali, m'mene analuka korona waminga anamveka pamutu pake, namfunda Iye malaya achibakuwa; 3#Mat. 27.29nadza kwa Iye, nanena, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda! Nampanda khofu. 4#Yoh. 18.38; 19.6Ndipo Pilato anatulukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa Iye chifukwa chilichonse. 5Pamenepo Yesu anatuluka kunja, atavala korona waminga, ndi malaya achibakuwa. Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu! 6#Mac. 3.13-15Ndipo pamene ansembe aakulu ndi anyamata anamuona Iye, anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni. Pilato ananenana nao, Mtengeni Iye inu nimumpachike; pakuti ine sindipeza chifukwa mwa Iye. 7#Lev. 24.16; Mat. 26.65Ayuda anamyankha iye, Tili nacho chilamulo ife, ndipo monga mwa chilamulocho ayenera kufa, chifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu. 8Ndipo pamene Pilato anamva mau awa, anaopa koposa. 9#Yes. 53.7; Mat. 27.12, 14Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankha kanthu. 10Chifukwa chake Pilato ananena kwa Iye, Simulankhula ndi ine kodi? Simudziwa kodi kuti ulamuliro ndili nao wakukumasulani, ndipo ndili nao ulamuliro wakukupachikani? 11#Luk. 22.53Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa. 12#Luk. 23.2; Mac. 17.7Pa ichi Pilato anafuna kumasula Iye; koma Ayuda anafuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara. 13Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lake, Bwalo lamiyala, koma m'Chihebri, Gabata. 14Koma linali tsiku lokonza Paska; panali monga ora lachisanu ndi chimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, mfumu yanu! 15#Gen. 49.10Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara. 16#Mat. 27.26, 31Ndipo pamenepo anampereka Iye kwa iwo kuti ampachike.
Ampachika Yesu pamtanda
(Mat. 27.32-56; Mrk. 15.22-39; Luk. 23.33-47)
Pamenepo anatenga Yesu; 17#Mat. 27.33ndipo anasenza mtanda yekha, natuluka kunka kumalo otchedwa Malo a Bade, amene atchedwa m'Chihebri, Gologota: 18#Mat. 27.38kumene anampachika Iye; ndipo pamodzi ndi Iye awiri ena, chakuno ndi chauko, koma Yesu pakati. 19#Mat. 27.37Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA. 20Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; chifukwa malo amene Yesu anapachikidwapo anali pafupi pa mudziwo; ndipo linalembedwa m'Chihebri, ndi m'Chilatini, ndi m'Chigriki. 21Pamenepo ansembe aakulu a Ayuda, ananena kwa Pilato, Musalembe, Mfumu ya Ayuda; koma kuti Iyeyu anati, Ndili mfumu ya Ayuda. 22Pilato anayankha, Chimene ndalemba, ndalemba.
23 #
Mat. 27.35
Pamenepo asilikali, m'mene adapachika Yesu, anatenga zovala zake, anadula panai, natenga wina china, wina china, ndiponso malaya; koma malaya anaombedwa monsemo kuyambira pamwamba pake, analibe msoko. 24#Mas. 22.18Chifukwa chake anati wina kwa mnzake, Tisang'ambe awa, koma tichite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zovala zanga mwa iwo okha, ndi pa malaya anga anachitira maere. Ndipo asilikali anachita izi. 25#Mat. 27.55Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Maria, mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa Magadala. 26#Yoh. 2.4; 13.23; 20.2Pamenepo Yesu pakuona amake, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu! 27Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amai wako. Ndipo kuyambira ora lomweli wophunzirayo ananka naye kwao.
28 #
Mas. 69.21
Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu. 29#Mat. 27.48Kunaikidwako chotengera chodzala ndi vinyo wosasayo pa phesi la hisope, nachifikitsa kukamwa kwake. 30#Yoh. 17.4Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.
Sathyola miyendo ya Yesu
31 #
Mrk. 15.42; Deut. 21.23 Pomwepo Ayuda, popeza panali tsiku lokonzera, kuti mitembo ingatsale pamtanda tsiku la Sabata, pakuti tsiku lomwelo la Sabata linali lalikulu, anapempha Pilato kuti miyendo yao ithyoledwe, ndipo achotsedwe. 32Chifukwa chake anadza asilikali nathyola miyendo ya woyambayo, ndi ya winayo wopachikidwa pamodzi ndi Iye; 33koma pofika kwa Yesu, m'mene anamuona Iye, kuti wafa kale, sanathyola miyendo yake; 34#1Yoh. 5.6, 8koma mmodzi wa asilikali anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yake, ndipo panatuluka pomwepo mwazi ndi madzi. 35#1Yoh. 1.1-3Ndipo iye amene anaona, wachita umboni, ndi umboni wake uli woona; ndipo iyeyu adziwa kuti anena zoona, kuti inunso mukakhulupirire. 36#Eks. 12.46Pakuti izi zinachitika, kuti lembo likwaniridwe, Fupa la Iye silidzathyoledwa. 37#Mas. 22.16-17; Zek. 12.10Ndipo linenanso lembo lina, Adzayang'ana pa Iye amene anampyoza.
Kuikidwa kwa Yesu
(Mat. 27.57-60; Mrk. 15.43-47; Luk. 23.50-56)
38 #
Mat. 27.57-58
Chitatha ichi Yosefe wa ku Arimatea, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akachotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Chifukwa chake anadza, nachotsa mtembo wake. 39#Yoh. 3.1-2Koma anadzanso Nikodemo, amene anadza kwa Iye usiku poyamba paja, alikutenga chisanganizo cha mure ndi aloe, monga miyeso zana. 40Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda. 41Koma kunali munda kumalo kumene anapachikidwako, ndi m'mundamo munali manda atsopano m'mene sanaikidwamo munthu aliyense nthawi zonse. 42#Yes. 53.9; Yoh. 19.31Pomwepo ndipo anaika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.
Atualmente selecionado:
YOHANE 19: BLPB2014
Destaque
Partilhar
Copiar
Quer salvar os seus destaques em todos os seus dispositivos? Faça o seu registo ou inicie sessão
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: