YOHANE 21
21
Yesu awaonekera kunyanja ya Tiberiasi
1Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa ophunzira ake kunyanja ya Tiberiasi. Koma anadzionetsera chotere.
2 #
Mat. 4.21; Yoh. 1.45 Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimo, ndi Natanaele wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedeo, ndi awiri ena a ophunzira ake. 3Simoni Petro ananena nao, Ndinka kukasodza. Ananena naye, Ifenso tipita nawe. Anatuluka, nalowa m'ngalawa; ndipo m'usiku muja sanagwira kanthu. 4#Yoh. 20.14Koma pakuyamba kucha, Yesu anaimirira pambali pa nyanja, komatu ophunzirawo sanadziwa kuti ndiye Yesu. 5#Luk. 24.41Yesu ananena nao, Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi? Anamyankha Iye, Iai. 6#Luk. 5.4, 6-7Koma anati kwa iwo, Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza. Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka chifukwa cha kuchuluka nsomba. 7#Yoh. 13.33Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadziveka malaya a pathupi, pakuti anali wamaliseche, nadziponya yekha m'nyanja. 8Koma ophunzira ena anadza m'kangalawa, pakuti sanali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana awiri, nakoka khoka la nsombazo. 9Ndipo pamene anatulukira pamtunda, anapenya moto wamakala pomwepo, ndi kansomba kosanjikikako, ndi mkate. 10Yesu ananena nao, Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano. 11Chifukwa chake Simoni Petro anakwera m'ngalawa nakokera khoka kumtunda lodzala ndi nsomba zazikulu, zana limodzi, ndi makumi asanu ndi zitatu; ndipo zingakhale zinachuluka kotere, kokha silinang'ambika. 12#Mac. 10.40-41Yesu ananena nao, Idzani mufisule. Koma palibe mmodzi wa ophunzira anatha kumfunsa Iye, Ndinu yani? Podziwa kuti ndiye Ambuye. 13Yesu anadza natenga mkate napatsa iwo, momwemonso nsomba. 14#Yoh. 20.19, 26Imeneyo ndi nthawi yachitatu yakudzionetsera Yesu kwa ophunzira ake, m'mene atauka kwa akufa.
15Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Dyetsa anaankhosa anga. 16#Mac. 20.28Ananena nayenso kachiwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga. 17#Yoh. 2.24-25Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga. 18#Yoh. 13.36; Mac. 12.3-4Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, pamene unali mnyamata unadzimangira wekha m'chuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzatulutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna. 19#2Pet. 1.14Koma ichi ananena ndi kuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m'mene ananena ichi, anati kwa iye, Nditsate Ine. 20#Yoh. 20.2Petro, m'mene anacheuka, anapenya wophunzira amene Yesu anamkonda alikutsata, amenenso anatsamira pachifuwa pake pamgonero, nati, Ambuye, ndani iye wakupereka Inu? 21#Mat. 16.27-28; 25.31; Chiv. 2.25; 22.7, 20Pamenepo Petro pakumuona, ananena kwa Yesu, Ambuye, koma nanga uyu? 22Yesu ananena naye, Ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza Ine, kuli chiyani ndi iwe? Unditsate Ine iwe. 23Chifukwa chake mau awa anatuluka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananena kwa iye kuti sadzafa; koma, Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli chiyani ndi iwe?
24 #
Yoh. 19.35
Yemweyu ndiye wophunzira wakuchita umboni za izi, ndipo analembera izi; ndipo tidziwa kuti umboni wake ndi woona.
25 #
Yoh. 20.30; Amo. 7.10 Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anazichita, zoti zikadalembedwa zonse phee, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo a mabuku amene akadalembedwa. Amen.
Atualmente selecionado:
YOHANE 21: BLPB2014
Destaque
Partilhar
Copiar
Quer salvar os seus destaques em todos os seus dispositivos? Faça o seu registo ou inicie sessão
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: