LUKA 14
14
Yesu achiritsa munthu wambulu
1Ndipo panali pamene Iye analowa m'nyumba ya mmodzi wa akulu a Afarisi tsiku la Sabata, kukadya, iwo analikumzonda Iye. 2Ndipo onani, panali pamaso pake munthu wambulu. 3#Mat. 12.10Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai? 4Koma iwo anakhala chete. Ndipo anamtenga namchiritsa, namuuza apite. 5#Eks. 23.5; Deut. 22.4; Luk. 13.15Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi? 6Ndipo iwo sanathe kumbwezera mau pa zinthu izi.
Fanizo la mipando ya ulemu
7Ndipo Iye ananena fanizo kwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo, 8Pamene paliponse waitanidwa iwe ndi munthu ku chakudya cha ukwati, usaseama pa mpando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye, 9ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo. 10#Miy. 25.6-7Koma pamene paliponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pachakudya pamodzi ndi iwe. 11#Mas. 18.27; Mat. 23.12; Yak. 4.6Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.
12Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho. 13Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu; 14ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa olungama.
Fanizo la phwando lalikulu
(Mat. 22.1-14)
15 #
Chiv. 19.9
Ndipo pamene wina wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye anamva izi, anati kwa Iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu. 16Koma anati kwa iye, Munthu wina anakonza phwando lalikulu; naitana anthu ambiri; 17ndipo anatumiza kapolo wake pa nthawi ya phwando kukanena kwa oitanidwawo, Idzani, chifukwa zonse zakonzeka tsopano. 18Ndipo onse ndi mtima umodzi anayamba kuwiringula. Woyamba anati kwa iye, Ine ndagula munda, ndipo ndiyenera ndituluke kukauona; ndikupempha undilole ine ndisafika. 19Ndipo anati wina, Ine ndagula ng'ombe za magoli asanu, ndipo ndinka kukaziyesa; ndikupempha undilole ine ndisafika. 20Ndipo anati wina, Ine ndakwatira mkazi, ndipo chifukwa chake sindingathe kudza. 21Ndipo kapoloyo pakubwera anauza mbuye wake zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba anakwiya, nati kwa kapolo wake, Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mudzi, nubwere nao muno aumphawi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina. 22Ndipo kapoloyo anati, Ambuye, chimene munachilamulira chachitika, ndipo malo atsalapo. 23Ndipo mbuye ananena kwa kapoloyo, Tuluka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe, kuti nyumba yanga idzale. 24#Mat. 21.43; 22.8; Mac. 13.46Pakuti ndinena kwa inu, kuti kulibe mmodzi wa amuna oitanidwa aja adzalawa phwando langa.
Womtsata Ambuye adzayesedwa
(Mat. 10.37-39)
25Ndipo mipingo yambiri ya anthu inamuka naye; ndipo Iye anapotoloka, nati kwa iwo, 26Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga. 27#Mat. 16.24; 2Tim. 3.12Ndipo amene aliyense sasenza mtanda wake wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sakhoza kukhala wophunzira wanga.
28 #
Miy. 24.27
Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza? 29Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya kumaziko ake, osakhoza kuimaliza anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye, 30ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumaliza.
Fanizo la mfumu yanzeru
31Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzake, sathanga wakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikali ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikali zikwi makumi awiri? 32Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere. 33Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sakhoza kukhala wophunzira wanga. 34#Mat. 5.13Kotero mchere uli wokoma; koma ngati mchere utasukuluka adzaukoleretsa ndi chiyani? 35Suyenera kuuthira pamunda kapena padzala, autaya kunja. Amene ali nao makutu akumva amve.
Atualmente selecionado:
LUKA 14: BLPB2014
Destaque
Partilhar
Copiar
Quer salvar os seus destaques em todos os seus dispositivos? Faça o seu registo ou inicie sessão
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: