LUKA 21
21
Mphatso ya mkazi wamasiye
(Mat. 12.41-44)
1Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni chuma alikuika zopereka zao mosungiramo ndalama. 2Ndipo anaona mkazi wina wamasiye waumphawi alikuika momwemo timakobiri tiwiri. 3#2Ako. 8.12Ndipo Iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi anaikamo koposa onse; 4pakuti onse amenewa anaika mwa unyinji wao pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.
Yesu aneneratu zam'tsogolo, chiyambi cha masautso
(Mat. 24.1-14; Mrk. 13.1-13)
5Ndipo pamene ena analikunena za Kachisiyo, kuti anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, anati Iye, 6#Luk. 19.44Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala unzake, umene sudzagwetsedwa. 7Ndipo iwo anamfunsa Iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro ndi chiyani pamene izi ziti zichitike? 8#Mrk. 13.5Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao. 9Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mapanduko, musaopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kuchitika; koma mathedwe sakhala pomwepo.
10Pamenepo ananena nao, Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina: 11ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba. 12#Mrk. 13.9; Mac. 4.3; 5.18; 12.4; 16.24; 25.23; 1Pet. 2.13Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa. 13#Afi. 1.13, 28-29Kudzakhala kwa inu ngati umboni. 14#Mat. 10.19; Mrk. 13.11Chifukwa chake tsimikizani mumtima mwanu, kuti usanafike mlandu musalingirire chimene mudzayankha. 15#Mac. 6.10Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa. 16#Mik. 7.6; Mrk. 13.12; Mac. 7.59; 12.2Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a fuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani. 17#Mat. 10.22Ndipo anthu onse adzadana ndi inu chifukwa cha dzina langa. 18#Mat. 10.30Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu. 19Mudzakhala nao moyo wanu m'chipiriro.
Aneneratu za kupasuka kwa Yerusalemu
(Mat. 24.15-28; Mrk. 13.14-24)
20Koma pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipulumutso chake chayandikira. 21Pamenepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m'kati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumilaga asalowemo. 22Chifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zichitike. 23#Mat. 24.19Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! Pakuti padzakhala chisauko chachikulu padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa. 24#Dan. 9.27; 12.7; Aro. 11.25Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.
Za kubwera kwa Mwana wamunthu
(Mat. 24.29-35; Mrk. 13.24-31)
25 #
2Pet. 3.10, 12 Ndipo kudzakhala zizindikiro pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi pa dziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkukumo wake wa nyanja ndi mafunde ake; 26anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza kudziko lapansi; pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. 27#Chiv. 1.7; 14.14Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa Munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. 28#Aro. 8.19, 23Koma poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiomboledwe chanu chayandikira. 29#Mrk. 13.28Ndipo ananena nao fanizo; Onani mkuyu, ndi mitengo yonse: 30pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja lili pafupi pomwepo. 31Inde chotero inunso, pakuona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. 32Indetu ndinena ndinu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitachitika. 33Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.
Khalani odikira
(Mat. 24.36-44; Mrk. 13.33-37)
34 #
Aro. 13.13
Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; 35#1Ate. 5.2-4pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi. 36#Mrk. 13.33Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu.
37 #
Luk. 22.39; Yoh. 8.1-2 Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa m'Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona pa phiri lotchedwa la Azitona. 38Ndipo anthu onse analawira mamawa kudza kwa Iye ku Kachisi kudzamvera Iye.
Atualmente selecionado:
LUKA 21: BLPB2014
Destaque
Partilhar
Copiar
Quer salvar os seus destaques em todos os seus dispositivos? Faça o seu registo ou inicie sessão
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: