GENESIS 16

16
Sarai ndi Hagara
1Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu sanambalire iye mwana; ndipo anali ndi mdzakazi, wa ku Ejipito, dzina lake Hagara. 2Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Taonanitu, Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: lowanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana. Ndipo Abramu anamvera mau a Sarai. 3Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wake wa ku Ejipito, Abramu atakhala m'dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wake, kuti akhale mkazi wake. 4Ndipo analowa kwa Hagara, ndipo iye anatenga pakati. Pamene anaona kuti anatenga pakati, anapeputsa wakuka wake m'maso mwake. 5#1Sam. 24.12Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine. 6Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umchitire iye chimene chikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwake. 7Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'chipululu, pa kasupe wa pa njira ya ku Suri. 8Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wake wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwake kwa wakuka wanga Sarai. 9Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Bwera kwa wakuka wako, udzichepetse wekha pamanja pake. 10#Gen. 17.20Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndidzachulukitsa ndithu mbeu zako, kuti unyinji wao sudzawerengeka.
Kubadwa kwa Ismaele
11Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako. 12#Gen. 25.18; Mac. 7.8Ndipo iye adzakhala munthu wa m'thengo; ndipo dzanja lake lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ake onse. 13Ndipo anatcha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang'ana pambuyo pake pa Iye amene wakundiona ine? 14Chifukwa chake chitsimecho chinatchedwa Beere-Lahai-Roi; taonani chili pakati pa Kadesi ndi Beredi. 15Ndipo Hagara anambalira Abramu mwana wamwamuna ndipo Abramu anatcha dzina la mwana wake amene anambalira iye Hagara, Ismaele. 16Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi, pamene Hagara anambalira Abramu Ismaele.

Märk

Dela

Kopiera

None

Vill du ha dina höjdpunkter sparade på alla dina enheter? Registrera dig eller logga in