GENESIS 18
18
Amithenga atatu amuonekera Abrahamu
1Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamure, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuwa. 2#Aheb. 13.2Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati, 3Mbuyanga, ngatitu ndi ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu; 4nditengetu madzi pang'ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo; 5ndipo ndidzatenga chakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena. 6Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wake kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate. 7Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng'ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika. 8Ndipo anatenga mafuta amkaka, ndi mkaka, ndi kamwana ka ng'ombe kamene anaphika, naziika patsogolo pao; ndipo iye anaimirira iwo patsinde pa mtengo, ndipo anadya. 9Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Taonani m'hemamo. 10#Gen. 17.19, 21; 21.2Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yake; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pake. 11#Aro. 4.19; Aheb. 11.11-12Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, anapitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumachita ndi akazi; 12ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba? 13Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba? 14#Yer. 32.17; Mat. 19.26; Luk. 1.37Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna. 15Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; chifukwa anaopa. Ndipo anati, Iai; koma unaseka. 16Ndipo anthuwo anauka kuchokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza. 17#Amo. 3.7Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu chimene ndichita? 18#Gen. 12.3; Mac. 3.25; Agal. 3.8Pakuti Abrahamu adzakhala ndithu wamkulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsika mwa iye? 19#Amo. 3.2Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye. 20#Yes. 3.9; Yak. 5.4Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukulu, ndipo popeza kuchimwa kwao kuli kulemera ndithu, 21#Eks. 3.8ndidzatsikatu ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziwa.
Abrahamu apempherera a ku Sodomu
22 #
Mas. 106.23
Ndipo anthuwo anatembenuka nachoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova. 23#Num. 16.22; 2Sam. 24.17Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa? 24Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi; kodi mudzaononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo? 25#Deut. 32.4; Aro. 3.5-6Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi? 26#Yes. 65.8; Ezk. 22.30Ndipo anati Yehova, Ndikapeza m'Sodomu olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi, ndidzasiya malo onse chifukwa cha iwo. 27Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa: 28kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mudzi wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga. 29Ndipo ananenanso kwa Iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi anai. 30Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzachita. 31Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi awiri. 32Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi. 33Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.
Nu markerat:
GENESIS 18: BLPB2014
Märk
Dela
Kopiera
Vill du ha dina höjdpunkter sparade på alla dina enheter? Registrera dig eller logga in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi