GENESIS 23
23
Imfa ndi kuikidwa kwa Sara
1Ndipo Sara anali wa zaka zana limodzi kudza makumi awiri ndi zisanu ndi ziwiri: ndizo zaka za moyo wa Sara. 2Ndipo Sara anafa m'Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire. 3Ndipo Abrahamu anauka pa wakufa wake, nanena kwa ana a Hiti, nati, 4#Mac. 7.5Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso. 5Ndipo ana a Hiti anayankha Abrahamu nati kwa iye, 6Mutimvere ife mfumu, ndinu kalonga wamkulu pakati pa ife; muike wakufa wanu m'manda mwathu mosankhika: palibe munthu yense wa ife adzakaniza manda ake, kuti muike wakufa wanu. 7Ndipo anauka Abrahamu naweramira anthu a m'dzikomo, ana a Hiti. 8Ndipo ananena nao, kuti, Ngati mukandivomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efuroni mwana wake wa Zohari, 9kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene lili pansonga pa munda wake; pa mtengo wake wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda. 10#Rut. 4.1Ndipo Efuroni anakhala pakati pa ana a Hiti: ndipo Efuroni Muhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Hiti, onse amene analowa pa chipata cha mudzi wake, kuti, 11Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga lili m'menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu. 12Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m'dzikomo. 13Ndipo ananena kwa Efuroni alinkumva anthu a m'dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wake wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m'menemo. 14Ndipo Efuroni anamyankha Abrahamu, nati kwa iye, 15Mfumu, mundimvere ine; kadziko ka mtengo wake wa masekeli a siliva mazana anai, ndiko chiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani wakufa wanu. 16#Gen. 50.13Ndipo Abrahamu anamvera Efuroni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efuroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Hiti, masekeli a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda. 17Ndipo munda wa Efuroni umene unali m'Makipela, umene unali patsogolo pa Mamure, munda ndi phanga lili momwemo, ndi mitengo yonse inali m'mundamo, yokhala m'malire monse mozungulira momwemo, 18inalimbitsidwa kwa Abrahamu ikhale yake, pamaso pa ana a Hiti, pa onse amene analowa pa chipata cha mudzi wake. 19Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wake m'phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamure (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani. 20Ndipo ana a Hiti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga lili m'menemo, likhale lake lamanda.
Nu markerat:
GENESIS 23: BLPB2014
Märk
Dela
Kopiera
Vill du ha dina höjdpunkter sparade på alla dina enheter? Registrera dig eller logga in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi