Gen. 10

10
Mibadwo ya ana a Nowa
(1 Mbi. 1.5-23)
1Nayi mibadwo ya ana a Nowa: Semu, Hamu ndi Yafeti. Atatu ameneŵa adabereka ana ao chitatha chigumula chija.
2Ana a Yafeti anali Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Meseki ndi Tirasi. 3Ana a Gomeri anali Asikenazi, Rifati ndi Togarima. 4Ana a Yavani anali Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Dodanimu. 5Iwoŵa ndiwo anali makolo a onse amene ankakhala m'mbali mwa nyanja, ndi pa zilumba zam'nyanja. Ameneŵa ndiwo ana a Yafeti. Mafuko ao anali osiyanasiyana, ndipo ankakhala m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake.
6Ana a Hamu anali Kusi, Ejipito, Libia ndi Kanani. 7Ana a Kusi anali Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani. 8Kusi adabereka Nimirodi. Nimirodi anali wankhondo woyamba wanyonga pa dziko lapansi. 9Iyeyu analinso mlenje wamkulu pamaso pa Chauta. Nchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo chakuti, “Ndiwe mlenje wamkulu pamaso pa Chauta, ngati Nimirodi.” 10Ankalamulira ku Babiloni, ku Ereki, ndi ku Akadi. Maufumu onseŵa anali m'dziko la Sinara. 11Iyeyu adachoka ku Sinara nakakhala ku Asiriya, ndipo adakamanga mizinda ya Ninive, Rehobotiiri, Kala, 12ndi mzinda wa Reseni umene uli pakati pa Ninive ndi mzinda waukulu uja wa Kala. 13Ejipito ndi amene anali kholo la anthu a ku Ludi, Anamu, Lehabu, Nafutu, 14Patirusi, Kasilu ndi Kafitori, makolo a Afilisti.
15Kanani adabereka mwana wake wachisamba dzina lake Sidoni, ndipo adaberekanso Heti. 16Ameneŵa adabereka Ayebusi, Aamori, Agirigasi. 17Ahivi, Aariki, Asini, 18Aaravadi, Azemari ndi Ahamati. Pambuyo pake mafuko a Akananiwo adabalalika ponseponse, 19mpaka ku malire a Kanani. Malirewo adayambira ku Sidoni namaloŵa ku Gerari mpaka ku Gaza ndi kumaloŵanso ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa. 20Ameneŵa ndiwo ana a Hamu ndipo ankakhala m'mafuko osiyanasiyana, ndi m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake.
21Semu ndiye kholo la ana onse a Eberi, ndiponso ndiye mkulu wake wa Yafeti. Iyeyu anali ndi ana. 22Ana a Semu anali Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu. 23Ana a Aramu anali Uzi, Hulu, Getere ndi Masi. 24Aripakisadi adabereka Sela, ndipo Sela adabereka Eberi. 25Eberi anali ndi ana aŵiri. Wina anali Pelegi, chifukwa pa nthaŵi ya moyo wake, anthu onse a pa dziko lapansi anali ogaŵikana. Dzina la mbale wake linali Yokotani. 26Yokotani adabereka Alimodadi, Selefi, Hazara-Maveti, Yera, 27Hadoramu, Uzali, Dikila, 28Obala, Abimaele, Sheba, 29Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onseŵa anali ana a Yokotani. 30Dziko limene ankakhalamo lidayambira ku Mesa kumaloŵa ku Sefari ku mapiri chakuvuma. 31Ameneŵa ndiwo zidzukulu za Semu. Mafuko ao anali osiyanasiyana, ndipo ankakhalanso m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake.
32Onseŵa ndiwo mafuko a zidzukulu za Nowa potsata mibadwo yao ndi mitundu yao. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idatuluka mwa mafuko a Nowa ameneŵa, chitatha chigumula chija.

Поточний вибір:

Gen. 10: BLY-DC

Позначайте

Поділитись

Копіювати

None

Хочете, щоб ваші позначення зберігалися на всіх ваших пристроях? Зареєструйтеся або увійдіть