Genesis 5
5
Mibado Kuyambira pa Adamu Mpaka Nowa
1Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi:
Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu. 2Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha “Munthu.”
3Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti. 4Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 5Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira.
6Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi. 7Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 8Zaka zonse za Seti zinali 912 ndipo anamwalira.
9Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani. 10Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 11Zaka zonse za Enosi pamodzi zinali 905 ndipo anamwalira.
12Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli. 13Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 14Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira.
15Pamene Mahalaleli anali ndi zaka 65, anabereka Yaredi. 16Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 17Zaka zonse za Mahalaleli zinali 895 ndipo anamwalira.
18Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki. 19Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 20Zaka zonse za Yaredi zinali 962 ndipo anamwalira.
21Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela. 22Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 23Zaka zonse za Enoki zinali 365. 24Enoki anayenda ndi Mulungu; ndipo iye sanaonekenso chifukwa Mulungu anamutenga.
25Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki. 26Ndipo atabadwa Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka zina 782 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 27Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira.
28Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. 29Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, “Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.” 30Atabadwa Nowa, Lameki anakhala zaka zina 595 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 31Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira.
32Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti.
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.