የYouVersion አርማ
የፍለጋ አዶ

GENESIS 6:1-4

GENESIS 6:1-4 BLPB2014

Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana akazi anawabadwira iwo, kuti ana amuna a Mulungu anayang'ana ana akazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha. Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri. Pa dziko lapansi panali anthu akulukulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.