GENESIS 6
6
Kulowerera kwa mtundu wa anthu
1Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana akazi anawabadwira iwo, 2kuti ana amuna a Mulungu anayang'ana ana akazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha. 3#Neh. 9.30; Agal. 5.16-17; Yud. 14Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri. 4Pa dziko lapansi panali anthu akulukulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka. 5#Gen. 6.9; Mik. 6.8; Mali. 2.6; Aheb. 11.5Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha. 6#1Sam. 15.11; Yes. 63.10; Aef. 4.30Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anavutika m'mtima mwake. 7Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo. 8#Eks. 33.12Koma Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova.
9 #
Gen. 5.22
Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu. 10Ndipo Nowa anabala ana amuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti. 11Ndipo dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa. 12Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao pa dziko lapansi.
Chigumula
13 #
Ezk. 7.2-3
Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi. 14Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale; upangemo zipinda m'chingalawamo, ndipo upake ndi utoto m'kati ndi kunja. 15Kupanga kwake ndi kotere: m'litali mwake mwa chingalawa mikono mazana atatu, m'mimba mwake mikono makumi asanu, m'msinkhu mwake mikono makumi atatu. 16Uike zenera m'chingalawacho, ulimalize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pake: khomo la chingalawa uike m'mbali mwake; nuchipange ndi nyumba yapansi, ndi yachiwiri, ndi yachitatu. 17#2Pet. 2.5Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi pa dziko lapansi, kuti chiononge zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo pansi pa thambo; zinthu zonse za m'dziko lapansi zidzafa. 18Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe. 19Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiriziwiri za mtundu wao ulowetse m'chingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi. 20Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiriziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo. 21Ndipo iwe udzitengereko wekha zakudya zonse zodyedwa, nudzisonkhanitsire izi wekha: ndipo zidzakhala zakudya za iwe ndi za iwo. 22#Aheb. 11.7Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.
Currently Selected:
GENESIS 6: BLPB2014
ማድመቅ
Share
Copy
ያደመቋቸው ምንባቦች በሁሉም መሣሪያዎችዎ ላይ እንዲቀመጡ ይፈልጋሉ? ይመዝገቡ ወይም ይግቡ
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi