Yesu ataona amayi ake pamenepo ndi wophunzira amene Iye anamukonda atayima pafupipo, Iye anati kwa amayi ake, “Amayi nayu mwana wanu.” Anawuzanso wophunzirayo kuti, “Nawa amayi ako.” Kuyambira nthawi imeneyo, wophunzirayo anatenga amayiwo kupita nawo kwawo.