Pakuti lembo litere, Amene aliyense akhulupirira Iye, sadzachita manyazi. Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mgriki; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa Iye; pakuti, amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.