YouVersion Logo
Search Icon

AROMA 10

10
Ayuda anataya chilungamo cha Mulungu
1Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke. 2#Mac. 21.20Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso. 3#Aro. 9.31Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonja ku chilungamo cha Mulungu. 4#Agal. 3.24Pakuti Khristu ali chimaliziro cha lamulo kulinga kuchilungamo kwa amene aliyense akhulupirira. 5#Lev. 18.5Pakuti Mose walemba kuti munthu amene achita chilungamo cha m'lamulo, adzakhala nacho ndi moyo.
6 # Deut. 30.12-13 Koma chilungamo cha chikhulupiriro chitero, Usamanena mumtima mwako, Adzakwera ndani Kumwambako? Ndiko, kutsitsako Khristu; 7kapena, Adzatsikira ndani ku chiphompho chakuya? Ndiko, kukweza Khristu kwa akufa, 8#Deut. 30.14Koma chitani? Mau ali pafupi ndiwe, m'kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mau a chikhulupiriro, amene ife tiwalalikira: 9#Mat. 10.32kuti ngati udzavomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka: 10pakuti ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi m'kamwa avomereza kutengapo chipulumutso. 11#Yer. 17.7; Aro. 9.33Pakuti lembo litere, Amene aliyense akhulupirira Iye, sadzachita manyazi. 12#Mac. 15.9Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mgriki; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa Iye; 13#Yow. 2.32; Mac. 2.21pakuti, amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka. 14Ndipo iwo adzaitana bwanji pa Iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji Iye amene sanamva za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? 15#Yes. 52.7; Nah. 1.15Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.
16 # Yes. 53.1 Koma sanamvera Uthenga Wabwino onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye, anakhulupirira ndani zonena ife? 17Chomwecho chikhulupiriro chidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Khristu. 18#Mas. 19.4; Akol. 1.23Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu,
Liu lao linatulukira kudziko lonse lapansi,
ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.
19 # Deut. 32.21 Koma nditi, Kodi Israele alibe kudziwa? Poyamba Mose anena,
Ine ndidzachititsa inu nsanje ndi iwo
amene sakhala mtundu wa anthu,
ndidzakwiyitsa inu ndi mtundu wopulukira.
20 # Yes. 65.1 Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati,
Ndinapezedwa ndi iwo amene sanandifuna;
ndinaonekera kwa iwo amene sanandifunsa.
21 # Yes. 65.2 Koma kwa Israele anena, Dzuwa lonse ndinatambalitsira manja anga kwa anthu osamvera ndi okanakana.

Currently Selected:

AROMA 10: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in