YouVersion Logo
Search Icon

Luka 23

23
1Kenaka gulu lonse la anthuwo linayimirira ndi kumutengera kwa Pilato. 2Ndipo iwo anayamba kumuneneza nati, “Ife tinapeza munthu uyu akusokoneza anthu a mtundu wathu ndipo amatsutsa zopereka msonkho kwa Kaisara komanso amati ndi Khristu, Mfumu.”
3Pamenepo Pilato anamufunsa Yesu kuti, “Kodi Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda?”
Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.”
4Kenaka Pilato anawawuza akulu a ansembe ndi gulu la anthu, “Ine sindikumupeza cholakwa munthuyu.”
5Koma iwo analimbikirabe kuti, “Iyeyu amasokoneza anthu ku Yudeya konse ndi chiphunzitso chake, Iyeyu anayambira ku Galileya ndipo wayenda mtunda wonse mpaka kuno.”
6Pakumva zimenezi, Pilato anafunsa ngati munthuyo ndi Mgalileya. 7Iye atamva kuti Yesu anali pansi pa ulamuliro wa Herode, anamutumiza kwa Herodeyo, amene pa nthawi imeneyo analinso mu Yerusalemu.
8Herode ataona Yesu, anakondwa kwambiri, chifukwa kwa nthawi yayitali, ankafunitsitsa atamuona. Kuchokera pa zimene anamva za Iye, anayembekezera kuti achita zodabwitsa. 9Iye anamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sanayankhe. 10Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anayimirira pamenepo ndi kumuneneza kwambiri. 11Pamenepo Herode ndi asilikali ake anamuseka ndi kumunyoza Iye. Atamuveka mkanjo wonyezimira, anamutumizanso kwa Pilato. 12Tsiku limenelo, Herode ndi Pilato anakhala abwenzi. Zisanachitike izi anali adani.
13Pilato anasonkhanitsa akulu a ansembe, oweruza ndi anthu, 14ndipo anawawuza kuti, “Munabweretsa munthuyu kwa ine ngati ndiye amawuza anthu kuti awukire. Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinapeze chomuyimbira mlandu. 15Herodenso sanapeze chifukwa pakuti wamutumizanso kwa ife monga mmene mukuoneramu. Iyeyu sanachite chinthu chakuti aphedwe. 16Nʼchifukwa chake, ine ndingomulanga, nʼkumumasula.” 17(Pa nthawi yachikondwerero cha Paska iye ankayenera kumasula munthu mmodzi).
18Onse pamodzi anafuwula kuti, “Muchotseni munthuyu! Timasulireni Baraba!” 19(Baraba anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe mu mzinda ndi kupha).
20Pofuna kumumasula Yesu, Pilato anawadandaulira iwo. 21Koma iwo anapitirirabe kufuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”
22Kachitatu anawafunsanso iwo kuti, “Chifukwa chiyani? Kodi munthu uyu wachita choyipa chanji? Ine sindinapeze cholakwa mwa Iye chakuti aphedwe choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.”
23Koma ndi mawu ofuwulitsa, analimbikirabe kuti Iye apachikidwe, ndipo kufuwulako kunapitirira. 24Choncho Pilato anatsimikiza kuchita zofuna zawozo. 25Iye anawamasulira munthu amene anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe ndi kupha, amene ankamufunayo, ndipo anawapatsa Yesu mwakufuna kwawo.
Kupachikidwa kwa Yesu
26Ndipo pamene ankapita naye, anagwira Simoni wa ku Kurene, amene ankachokera ku munda, namusenzetsa mtanda namuyendetsa pambuyo pa Yesu. 27Gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye, kuphatikiza amayi amene ankabuma ndi kumulirira. 28Yesu anatembenuka nati kwa iwo, “Ana aakazi a Yerusalemu, musandilirire Ine; dzililireni nokha ndi ana anu. 29Pakuti nthawi idzabwera imene inu mudzati, ‘Ndi odala amayi osabereka, mimba zimene sizinabereke ndi mawere amene sanayamwitse!’ 30Kenaka,
“adzawuza mapiri kuti tigwereni ife;
zitunda kuti tiphimbeni ife.
31 Chifukwa ngati anthu akuchita izi pa mtengo wauwisi, chidzachitike nʼchiyani ndi wowuma?”
32Amuna ena awiri, onsewo achifwamba, anatengedwanso pamodzi ndi Yesu kukaphedwa. 33Pamene anafika pamalo otchedwa Bade, anamupachika Iye pamodzi ndi achifwambawo, mmodzi kudzanja lake lamanja ndi winayo la ku lamazere. 34Yesu anati, “Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.” Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.
35Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, “Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.”
36Asilikalinso anabwera ndi kumunyoza Iye. Iwo anamupatsa vinyo wosasa, 37ndipo anati, “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.”
38Ndipo panalembedwa chikwangwani pamwamba pake chimene chinati: uyu ndi mfumu ya ayuda.
39Mmodzi wa achifwambawo, amene anapachikidwa, anamunenera Iye zamwano nati, “Kodi sindiwe Khristu? Dzipulumutse wekha ndi ifenso!”
40Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, “Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi? 41Ife tikulangidwa mwachilungamo, pakuti ife tikulandira monga mwa ntchito zathu. Koma munthu uyu sanachimwe kanthu.”
42Kenaka anati, “Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu.”
43Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso.”
Imfa ya Yesu
44Linali tsopano pafupi ora lachisanu ndi chimodzi, ndipo mdima unagwa pa dziko lonse mpaka ora lachisanu ndi chinayi, 45pakuti dzuwa linaleka kuwala. Ndipo chinsalu cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati. 46Yesu anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.” Atanena zimenezi, anamwalira.
47Kenturiyo, ataona zimene zinachitikazi, analemekeza Mulungu ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali munthu wolungama.” 48Anthu onse amene anasonkhana kudzaonerera izi, ataona zinachitikazo, anadziguguda pachifuwa ndipo anachoka. 49Koma onse amene anamudziwa Iye, kuphatikiza amayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya, anayimirira akuona zinthu izi.
Yesu Ayikidwa Mʼmanda
50Ndipo taonani panali munthu wina wotchedwa Yosefe, mmodzi wa gulu loweruza, munthu wabwino ndi wolungama. 51Iye sanavomereze zimene anzake abwalo anagwirizana ndi kuchita. Iye ankachokera ku mudzi wa Arimateyu wa ku Yudeya ndipo ankayembekezera ufumu wa Mulungu. 52Atapita kwa Pilato, iye anakapempha mtembo wa Yesu. 53Ndipo anawutsitsa, nawukulunga nsalu yabafuta nawuyika mʼmanda wosemedwa mʼmwala, amene panalibe wina amene anayikidwamo. 54Linali tsiku lokonzekera ndipo Sabata linatsala pangʼono kuyamba.
55Amayi amene anabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anatsata Yosefe ndipo anaona manda ndi momwe mtembo wake anawuyikira. 56Kenaka anapita ku mudzi ndi kukakonza mafuta onunkhira. Koma anapuma pa tsiku la Sabata pomvera malamulo.

Currently Selected:

Luka 23: CCL

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in