GENESIS 30
30
1Pamene Rakele anaona kuti sanambalire Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe. 2Ndipo Yakobo anapsa mtima ndi Rakele; nati, Kodi ine ndikhala m'malo a Mulungu amene akukaniza iwe zipatso za mimba? 3Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye. 4Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wake akhale mkazi wake; ndipo Yakobo analowa kwa iye. 5Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna. 6Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani. 7Ndipo Biliha mdzakazi wake wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri. 8Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkulu wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamutcha dzina lake Nafutali. 9Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wake, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake. 10Ndipo Zilipa mdzakazi wake wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna. 11Ndipo Leya anati, Wamwai ine! Ndipo anamutcha dzina lake Gadi. 12Ndipo Zilipa mdzakazi wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri. 13#Luk. 1.48Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana akazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere. 14#Nyi. 7.13Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m'thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako. 15Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako. 16Ndipo Yakobo anadza madzulo kuchokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo. 17Ndipo Mulungu anamvera Leya, ndipo anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu. 18Ndipo Leya anati, Mulungu wandipatsa ine mphotho yanga, chifukwa ndapatsa mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga: namutcha dzina lake Isakara. 19Ndipo Leya anatenganso pakati nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu ndi chimodzi. 20Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndambalira iye ana amuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamutcha dzina lake Zebuloni. 21Pambuyo pake ndipo anabala mwana wamkazi, namutcha dzina lake Dina. 22Ndipo Mulungu anakumbukira Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m'mimba mwake. 23Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, nati, Mulungu wachotsa manyazi anga; 24namutcha dzina lake Yosefe; ndipo anati, Yehova anandionjezera ine mwana wamwamuna wina.
Labani apangana ndi Yakobo
25Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa. 26Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe. 27Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, chifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine chifukwa cha iwe. 28Ndipo iye anati, Undipangire ine malipiro ako, ndipo ndidzakupatsa. 29Ndipo iye anati kwa Labani, Udziwa iwe chomwe ndakutumikira iwe ndi chomwe zachita zoweta zako ndi ine. 30Chifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zachuluka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kulikonse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa? 31Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandichitira ine chotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako. 32Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse kusankhasankha m'menemo zoweta zonse zamathothomathotho ndi zamawangamawanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamawangamawanga ndi zamathothomathotho: zotero zidzakhala malipiro anga. 33Chotero chilungamo changa chidzandivomereza m'tsogolo pamene udzandifika chifukwa cha malipiro amene ali patsogolo pako: iliyonse yosakhala yamathothomathotho ndi yamawangamawanga ya mbuzi, ndi iliyonse ya nkhosa yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba. 34Ndipo Labani anati, Taona, kukhale monga mau ako. 35Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde amene anali amipyololomipyololo ndi amathothomathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamawangamawanga ndi zamathothomathotho zonse zinali zoyera pang'ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m'dzanja la ana ake amuna. 36Ndipo iye yekha anatalikitsana ndi Yakobo ulendo wa masiku atatu: ndipo Yakobo anadyetsa ziweto zina za Labani. 37Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wowisi walibne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m'menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m'nthyolemo. 38Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'michera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa. 39Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathothomathotho, ndi zamawangamawanga. 40Ndipo Yakobo analekanitsa anaankhosa naziika pa zoweta za kuti ziyang'anire zamipyololomipyololo, ndi zakuda zonse za m'zoweta za Labani. 41Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m'micheramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo. 42Koma pamene ziweto zinali zofooka, sanaziike zimenezo: ndipo zofooka, zinali za Labani, ndi zolimba zinali za Yakobo. 43Munthuyo ndipo analemera kwambiri, nali nazo zoweta zambiri, ndi akapolo aamuna ndi aakazi, ndi ngamira, ndi abulu.
Currently Selected:
GENESIS 30: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi