GENESIS 31
31
Yakobo afuna kwao nathawa nazo zake
1Ndipo anamva mau a ana ake a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m'zinthu zinali za atate wathu wapeza iye chuma ichi chonse. 2Ndipo Yakobo anaona nkhope ya Labani, taonani, siinamuonekera iye monga kale. 3#Gen. 28.15; 32.9Ndipo Yehova anati kwa Yakobo, Bwera ku dziko la atate wako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakhala ndi iwe. 4Ndipo Yakobo anatumiza naitana Rakele ndi Leya adze kubusa ku zoweta zake, 5ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekera ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine. 6Ndipo inu mudziwa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu. 7Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andichitire ine choipa. 8Akati chotero, Zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako, zoweta zonse zinabala zamathothomathotho; ndipo akati iye chotere, Zamipyololomipyololo zidzakhala malipiro ako, ziweto zonse zinabala mipyololomipyololo. 9Chomwecho Mulungu anazichotsa zoweta za atate wanu, nandipatsa ine. 10Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m'kulota, taonani, atonde okwera ziweto anali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga. 11Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m'kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano. 12#Eks. 3.7Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga: chifukwa ndaona zonse zimene Labani akuchitira iwe. 13#Gen. 28.18Ine ndine Mulungu wa ku Betele, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine chilumbiriro: tsopano uka, nuchoke m'dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako. 14#2Sam. 20.1; 1Maf. 12.16Ndipo Rakele ndi Leya anayankha, nati kwa iye, Kodi tili nalonso gawo kapena cholowa m'nyumba ya atate wathu? 15Kodi satiyesa ife alendo? Chifukwa anatigulitsa ife, nathanso kuononga ndalama zathu. 16Chifukwa kuti chuma chonse Mulungu anachichotsa kwa atate wathu ndi chathu ndi cha ana athu; tsono, zonse wakunenera iwe Mulungu, uchite. 17Ndipo anauka Yakobo nakweza ana ake ndi akazi ake pa ngamira; 18ndipo ananka nazo zoweta zake zonse, ndi chuma chake chonse anachisonkhanitsa, zoweta zake anaziona m'Padanaramu, kuti anke kwa Isaki atate wake ku dziko la Kanani. 19#Ezk. 21.21; Zek. 10.2Ndipo Labani ananka kukasenga nkhosa zake: ndipo Rakele anaba aterafi a atate wake. 20Ndipo Yakobo anathawa kwa Labani Mwaramu mobisika, m'mene sanamuuze iye kuti analinkuthawa. 21Ndipo anathawa iye ndi zonse anali nazo: ndipo anauka naoloka panyanja naloza nkhope yake iyang'anire kuphiri la Giliyadi.
Labani alondola wothawayo
22Tsiku lachitatu anamuuza Labani kuti Yakobo wathawa. 23Ndipo iye anatenga abale ake pamodzi naye, namlondola iye ulendo wa masiku asanu ndi awiri: nampeza iye paphiri la Giliyadi. 24Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa. 25Ndipo Labani anakomana naye Yakobo. Ndipo Yakobo anamanga hema wake m'phirimo: ndipo Labani ndi abale ake anamanga m'phiri la Giliyadi. 26Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wachitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga akazi, monga mikoli ya lupanga. 27Wathawanji iwe mobisika, ndi kundichokera kuseri, osandiuza ine, kuti ndikadakumukitsa iwe ndi kusekerera ndi nyimbo ndi lingaka ndi zeze? 28Ndipo sunandiloleza ine ndimpsompsone ana anga aamuna ndi aakazi? Wapusa iwe pakuchita chotero. 29M'dzanja langa muli mphamvu yakuchitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa. 30Tsono ungakhale ukadamuka chifukwa mtima wako ulinkukhumba nyumba ya atate wako, bwanji waba iwe milungu yanga? 31Ndipo anayankha Yakobo nati kwa Labani, Chifukwa ndinaopa: chifukwa kuti, ndinati, Kapena udzandilanda ine ana ako akazi. 32Aliyense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi moyo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako zili ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba. 33Ndipo Labani analowa m'hema wa Yakobo, ndi m'hema wa Leya, ndi m'mahema a adzakazi awiri aja; koma sanapeze. Ndipo anatuluka m'hema wa Leya nalowa m'hema wa Rakele. 34Ndipo Rakele anatenga aterafiwo nabisa pa chokhalira cha ngamira, nakhala pamenepo. Ndipo Labani anafunafuna m'hema monse, koma sanawapeze. 35Ndipo Rakele anati kwa atate wake, Asakwiye mbuyanga kuti sindingathe kuuka pamaso panu; chifukwa zochitika pa akazi zili pa ine. Ndipo Labani anafunafuna koma sanapeze aterafiwo. 36Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndachimwa chiyani? Uchimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga? 37Pakuti wafunafuna monse ndili nazo, kodi wapeza chiyani pa zinthu za m'nyumba mwako? Tafika nacho apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse awiri. 38Zaka makumi awiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye. 39#Eks. 22.12Chimene chinazomoledwa ndi chilombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; pa dzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana. 40Chotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku chisanu; tulo tanga tinachoka m'maso mwanga. 41Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako akazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi. 42#Mas. 124.1Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.
Labani apangana ndi Yakobo
43Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzachitira ine chiyani lero kwa ana anga akazi amenewa, kapena ana ao amene anabala? 44Tsopano tiyeni tipangane pangano, ine ndi iwe; likhale mboni pakati pa ine ndi iwe. 45#Gen. 28.18Ndipo Yakobo anatenga mwala, nauimiritsa. 46Ndipo Yakobo anati kwa abale ake, Sonkhanitsani miyala; ndipo anasonkhanitsa miyala nakundika mulu: ndipo anadya pamulupo. 47Ndipo Labani anatcha pamenepo Yegara-Sahaduta; koma Yakobo anatcha Galedi. 48Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Chifukwa chake anatcha dzina lake, Galedi; 49#Ower. 11.29, 34ndi Mizipa, chifukwa kuti anati, Yehova ayang'anire pakati pa ine ndi iwe, pamene tisiyana wina ndi mnzake. 50#Ower. 11.10Ukasautsa ana anga akazi, kapena ukatenga akazi kuonjezera pa ana anga, palibe munthu mmodzi ali nafe; taonani, Mulungu ndiye mboni yanga ndi yako. 51Ndipo Labani anati kwa Yakobo. Taona muluwu, taona choimiritsachi, ndachiimiritsa pakati pathu. 52Muluwu ndiwo mboni, choimiritsachi ndicho mboni, kuti ine sindidzapitirira pa muluwu kunka kwa iwe, ndipo iwe sudzapitirira pa muluwu ndi pa choimiritsachi kudza kwa ine kuti tichitirane zoipa. 53Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isaki. 54Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse. 55M'mamawa Labani anauka nampsompsona ana ake aamuna ndi aakazi, nawadalitsa: ndipo Labani anachoka, nabwera kumalo kwake.
Currently Selected:
GENESIS 31: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi