AROMA 12
12
Kudzipereka nsembe kwa Mulungu
1 #
Aro. 6.13, 16, 19 Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. 2#Aef. 1.18; 1Yoh. 2.15Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
3 #
Miy. 25.27
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro. 4#1Ako. 12.12Pakuti monga m'thupi limodzi tili nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo sizili nayo ntchito imodzimodzi; 5#1Ako. 10.17; 12.20, 27chomwecho ife, ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake, wina ndi wina. 6#Aro. 12.3Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro; 7kapena yakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako; 8kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.
Makhalidwe okoma otiyenera
9 #
Mas. 34.14; 1Tim. 1.5 Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino. 10#Afi. 2.3; Aheb. 13.1M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; 11musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; 12#Luk. 10.20; 21.19; Aef. 6.18; 1Pet. 2.19-20kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. 13#1Ako. 16.1Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. 14#Mat. 5.44Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. 15#1Ako. 12.26Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. 16#Mas. 131.1-2; Aro. 15.5Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. 17#Miy. 20.22Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. 18#Aro. 14.19Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. 19#Lev. 19.18; Deut. 32.35Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. 20#Mat. 5.44Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a moto pamutu pake. 21Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.
Currently Selected:
AROMA 12: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi