1
AROMA 12:2
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Compare
Explore AROMA 12:2
2
AROMA 12:1
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Explore AROMA 12:1
3
AROMA 12:12
kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.
Explore AROMA 12:12
4
AROMA 12:21
Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.
Explore AROMA 12:21
5
AROMA 12:10
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu
Explore AROMA 12:10
6
AROMA 12:9
Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.
Explore AROMA 12:9
7
AROMA 12:18
Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.
Explore AROMA 12:18
8
AROMA 12:19
Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.
Explore AROMA 12:19
9
AROMA 12:11
musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye
Explore AROMA 12:11
10
AROMA 12:3
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.
Explore AROMA 12:3
11
AROMA 12:17
Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.
Explore AROMA 12:17
12
AROMA 12:16
Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.
Explore AROMA 12:16
13
AROMA 12:20
Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a moto pamutu pake.
Explore AROMA 12:20
14
AROMA 12:14-15
Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira.
Explore AROMA 12:14-15
15
AROMA 12:13
Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.
Explore AROMA 12:13
16
AROMA 12:4-5
Pakuti monga m'thupi limodzi tili nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo sizili nayo ntchito imodzimodzi; chomwecho ife, ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake, wina ndi wina.
Explore AROMA 12:4-5
Home
Bible
Plans
Videos