Lk. 11
11
Yesu aphunzitsa za kupemphera
(Mt. 6.9-15; 7.7-11)
1Nthaŵi ina Yesu ankapemphera pamalo pena. Pamene adatsiriza, wophunzira wake wina adampempha kuti, “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera, monga Yohane Mbatizi adaphunzitsira ophunzira ake.” 2Yesu adati, “Pamene mukupemphera muziti,
“ ‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe.
Ufumu wanu udze.
3Mutipatse ife tsiku lililonse
chakudya chathu chamasikuwonse.
4Mutikhululukire ife machimo athu,
pakuti ifenso timakhululukira aliyense wotilakwira.
Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa.’ ”
5Adaŵauzanso kuti, “Tangoganizani: wina mwa inu ali ndi bwenzi lake, nkupita kunyumba kwake pakati pa usiku, nakamuuza kuti, ‘Iwe mnzanga, kodi ungakhale ndi buledi mtatu? 6Kwafika bwenzi langa, ali pa ulendo, ndipo ndilibe choti ndingampatse.’ 7Koma wam'nyumbayo nkuyankha kuti, ‘Usandivute, ndatseka kale pa khomo, ndipo ine ndi ana anga tagona, sindingadzukenso kuti ndikupatse bulediyo.’ 8Ndithu ndikunenetsa kuti adzauka nkumupatsa, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha khama la wopempha uja. Ndipo adzampatsa zonse zimene akusoŵa.
9“Motero ndikukuuzani kuti, Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani, ndipo adzakutsekulirani. 10Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira, amene amafunafuna, ndiye amapeza, ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira. 11Ndani mwa atatenu, mwana wake atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? 12Kapena atampempha dzira, iye nkumupatsa chinkhanira? 13Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene aŵapempha.”
Za Yesu ndi Belezebulu
(Mt. 12.22-30; Mk. 3.20-27)
14Tsiku lina Yesu ankatulutsa mzimu woipa woletsa munthu kulankhula. Mzimuwo utatuluka, munthu amene anali wosalankhulayo adayamba kulankhula, mwakuti anthu ambirimbiri amene anali pomwepo adazizwa kwabasi. 15#Mt. 9.34; 10.25Koma ena mwa iwo adati, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipazi nzochokera kwa Belezebulu, mkulu wa mizimu yoipayo.” 16#Mt. 12.38; 16.1; Mk. 8.11Enanso pofuna kumuyesa, adampempha kuti aŵaonetse chizindikiro chozizwitsa chochokera kumwamba.#11.16 Chizindikiro…chochokera kumwamba: Ndiye kuti chotsimikizira kuti Mulungu ndiye adamtuma. 17Koma Yesu adaadziŵa maganizo ao, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo m'banja akayamba kukangana, banjalo limapasuka. 18Tsono ngati a mu ufumu wa Satana ayamba kuukirana, Satanayo ufumu wake ungalimbe bwanji? Paja inu mukuti Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu. 19Ngati Ineyo ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu, nanga ophunzira anu amaitulutsa ndi mphamvu za yani? Nchifukwa chake ophunzira anu omwewo ndi amene adzakuweruzani kuti ndinu olakwa. 20Koma ngati Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Mulungu, ndiye kuti Mulungu wayamba kukhazikitsa ufumu wake pakati panu.
21“Munthu wamphamvu akamalonda nyumba yake ali ndi zida zankhondo, katundu wake amakhala pabwino. 22Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa, namgonjetsa, amalanda zida zimene ankazidalirazo, nkugaŵagaŵa katundu amene walandayo.
23 #
Mk. 9.40
“Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ngwotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ngwomwaza.
Za mzimu woipa wobwerera mwa munthu
(Mt. 12.43-45)
24“Mzimu woipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo opanda madzi, kufunafuna malo opumulirako. Ndipo ukapanda kuŵapeza, umati, ‘Ndibwerera kunyumba kwanga komwe ndidatuluka kuja.’ 25Tsono ukafika, umapeza m'nyumba muja muli mosesasesa ndi mokonza bwino. 26Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iŵiri yoipa koposa uwowo, kenaka yonseyo imaloŵa nkukhazikika momwemo. Choncho mkhalidwe wotsiriza wa munthu uja umaipa koposa mkhalidwe wake woyamba.”
Za kudala kwenikweni
27Pamene Yesu ankalankhula zimenezi, mai wina pakati pa anthu ambiri aja adakweza mau namuuza kuti, “Ngwodala mai amene adabalani nkukuyamwitsani.” 28Koma Yesu adati, “Iyai, odala ndi anthu amene amamva mau a Mulungu naŵagwiritsa ntchito.”
Anthu apempha chizindikiro chozizwitsa
(Mt. 12.38-42; Mk. 8.12)
29 #
Mt. 16.4; Mk. 8.12 Pamene anthu ankachulukirachulukira, Yesu adati, “Anthu a mbadwo uno ngoipa, amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzachiwona chizindikirocho, kupatula cha mneneri Yona chija. 30#Yon. 3.4Monga Yona uja anali chizindikiro kwa anthu a ku Ninive, chomwechonso Mwana wa Munthu adzakhala chizindikiro kwa anthu a mbadwo uno. 31#1Maf. 10.1-10; 2Mbi. 9.1-12 Pa tsiku lachiweruzo mfumukazi yakumwera ija idzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nidzaŵatsutsa. Paja iyo idaachita kuchokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva zolankhula zanzeru za mfumu Solomoni. Ndipotu pano pali woposa Solomoni amene. 32#Yon. 3.5 Pa tsiku lachiweruzo anthu a ku Ninive aja adzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzaŵatsutsa. Paja iwowo adaatembenuka mtima, atamva malaliko a Yona. Ndipotu pano pali woposa Yona amene.”
Za nyale ya thupi
(Mt. 5.15; 6.22-23)
33 #
Mt. 5.15; Mk. 4.21; Lk. 8.16 “Munthu sati akayatsa nyale, nkuiika m'chipinda chapansi kapena kuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, kuti anthu oloŵa m'nyumbamo aone kuŵala kwake. 34Maso ndiwo nyale zounikira thupi lako. Ngati maso ako ali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala kuŵala. Koma ngati maso ako sali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala mdima. 35Chenjera tsono kuti kuŵala kumene kuli mwa iwe kusasanduke mdima. 36Ngati kuŵala kukhala m'thupi monse, popanda mdima pena paliponse, apo thupi lonse lidzakhala loŵala, monga pamene nyale ikukuunikira ndi kuŵala kwake.”
Yesu adzudzula Afarisi ndi akatswiri a Malamulo
(Mt. 23.1-36; Mk. 12.38-40; Lk. 20.45-47)
37Pamene Yesu adatsiriza kulankhula, wina wa m'gulu la Afarisi adamuitana kuti akadye naye. Tsono Yesu adaloŵa m'nyumba nakakhala podyera. 38Mfarisiyo adadabwa poona kuti Yesu wayamba kudya osatsata mwambo wao wa kasambidwe ka m'manja. 39Koma Ambuye adamuuza kuti, “Inu Afarisi mumatsuka kunja kwa chikho ndi mbale, koma m'kati ndinu odzaza ndi zonyenga ndi zankhanza. 40Ndinu anthu opusa! Kodi Mulungu amene adapanga zakunja, si yemweyo adapanganso zam'kati? 41Popereka zachifundo kwa amphaŵi, muzipereka zimene zili m'kati, ndiye pamenepo zanu zonse zidzakhala zoyera.
42 #
Lev. 27.30
“Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, cha timbeu tokometsera chakudya, ndiponso cha mbeu zakudimba za mtundu uliwonse. Koma simulabadako kuchita chilungamo, kapena kukonda Mulungu. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo. 43Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yaulemu m'nyumba zamapemphero, ndiponso kuti anthu azikupatsani moni waulemu pa misika. 44Muli ndi tsoka, chifukwa muli ngati manda osazindikirika,#11.44: manda osazindikirika: Onani pa Num. 19.16. amene anthu amapondapo osadziŵa kanthu.”
45Apo katswiri wina wa Malamulo adati, “Aphunzitsi, mukamanena zimenezi, mukunyozatu ndi ife tomwe.” 46Yesu adati, “Muli ndi tsokanso, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wosautsa kunyamula, pamene inuyo simumkhudzako mpang'ono pomwe. 47Muli ndi tsoka, chifukwa mumamanga ziliza za aneneri, pamene ndi makolo anu omwe akale amene adapha aneneriwo. 48Apo mukutsimikiza kuti mukuvomereza ntchito za makolo anuwo, popeza kuti iwowo adapha aneneriwo, inuyo nkumamanga ziliza zao. 49Nchifukwa chake Nzeru ya Mulungu idati, ‘Ndidzaŵatumizira aneneri ndi atumwi, koma anthu adzapha ena mwa iwo, nkuzunza ena.’#11.49: Ndidzaŵatumizira…nkuzunza ena: Onani pa Yer. 7.25,26. 50Motero anthu amakono adzakhala ndi mlandu chifukwa cha aneneri onse amene adaphedwa chilengedwere dziko lapansi, 51#Gen. 4.8; 2Mbi. 24.20, 21kuyambira kuphedwa kwa Abele,#11.51: kuphedwa kwa Abele: Onani pa Gen. 4.8. mpaka kuphedwa kwa Zakariya#11.51: kuphedwa kwa Zakariya: Onani pa 1 Mbi. 24.20,21. amene adaphedwera m'Nyumba ya Mulungu pakati pa guwa la nsembe ndi malo opatulika kopambana. Ndithu ndikunenetsa kuti anthu amakono adzakhaladi ndi mlandu chifukwa cha ophedwawo.
52“Muli ndi tsoka, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mudalanda kiyi yotsekulira anthu nzeru. Inu nomwe sumudaloŵe, ndipo mudatsekereza amene ankafuna kuloŵa.”
53Pamene Yesu adatuluka m'nyumbamo, aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adayamba kumzonda ndi kumpanikiza ndi mafunso ambiri ozunguza. 54Cholinga chao chinali chofuna kumtapa m'kamwa.
Currently Selected:
Lk. 11: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi