Lk. 12
12
Yesu achenjeza za chiphamaso
1 #
Mt. 16.6; Mk. 8.15 Nthaŵi imeneyo nkuti chikhamu cha anthu zikwi ndi zikwi chikusonkhana, kotero kuti anthuwo ankangopondana. Yesu adayamba kulankhula ndi ophunzira ake poyamba, Adati, “Chenjerani ndi chofufumitsira buledi cha Afarisi, chimene chili chiphamaso. 2#Mk. 4.22; Lk. 8.17Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululuka, ndipo kalikonse kobisika kadzadziŵika. 3Nchifukwa chake zonse zimene mwalankhula pa mdima, zidzamveka poyera, ndipo zonse zimene mwanong'oneza anthu m'kati mwa nyumba, adzazilengeza pa bwalo.”
Za woyenera kumuwopa
(Mt. 10.28-31)
4“Ndikukuuzani inu, abwenzi anga, kuti musamaopa anthu. Iwo angathe kupha thupi lokha, koma pambuyo pake alibenso china choti angachitepo. 5Koma ndikuchenjezeni: amene muyenera kumuwopa ndi Mulungu. Iye atalanda moyo wa munthu, ali nazonso mphamvu za kumponya m'Gehena. Ndithu ndi ameneyo amene muzimuwopa.
6“Suja amagulitsa atimba asanu tindalama tiŵiri? Komabe Mulungu saiŵala ndi mmodzi yemwe. 7Ndipo tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.”
Za kuvomereza Khristu pamaso pa anthu
(Mt. 10.32-33; 12.32; 10.19-20)
8“Ndithu kunena zoona, aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso Mwana wa Munthune ndidzamuvomereza pamaso pa angelo a Mulungu. 9Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti sandidziŵa, Inenso Mwana wa Munthune ndidzamkana pamaso pa angelo a Mulungu kuti sindimdziŵa.
10 #
Mt. 12.32; Mk. 3.29 “Aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira, koma wonyoza Mzimu Woyera ndi mau achipongwe, Mulungu sadzamkhululukira.
11 #
Mt. 10.19, 20; Mk. 13.11; Lk. 21.14, 15 “Akadzakutengerani ku milandu ku nyumba zamapemphero, kapena kwa mafumu ndiponso kwa akulu a Boma, musati mudzavutike nkumati, ‘Kaya ndikayankha bwanji? Ndikanena chiyani?’ 12Popeza kuti Mzimu Woyera adzakudziŵitsani pa nthaŵi yomweyo zimene mudzayenera kunena.”
Fanizo la munthu wachuma wopusa
13Munthu wina pakati pa anthu onse aja adapempha Yesu kuti, “Aphunzitsi, takandiwuzirani mbale wanga kuti andigaŵireko chuma chamasiye.” 14Koma Yesu adati, “Munthu iwe, ndani adandipatsa ntchito yokuweruzani kapena kumakugaŵirani chuma chanu chamasiye?” 15Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”
16Tsono Yesu adaŵaphera fanizo. Adati, “Munthu wina wachuma m'munda mwake mudabereka dzinthu dzambiri. 17Ndiye iye uja adayamba kuganiza kuti, ‘Nditani, poti ndilibe mosungira dzinthu dzanga?’ 18Tsono adati, ‘Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga nkumanga zina zazikulu, ndipo ndidzasungira dzinthu dzanja dzonse ndi chuma changa m'menemo. 19#Mphu. 11.19Kenaka ndidzauza mtima wanga kuti, Iwe mtima wanga, uli ndi chuma chambiri chimene chidzakukwanira zaka zambiri. Upumule, uzidya, uzimwa ndi kusangalala!’ 20Koma Mulungu adamuuza kuti, ‘Wopusawe! Usiku womwe uno akulanda moyo wako. Nanga zonse zimene wadzisungirazi zidzakhala za yani?’ ” 21Potsiriza Yesu adati, “Zimatero ndi munthu amene amadziwunjikira chuma, koma sali wachuma konse pamaso pa Mulungu.”
Za kuda nkhaŵa
(Mt. 6.25-34)
22Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. 23Pakuti moyo umaposa chakudya, ndipo thupi limaposa zovala. 24Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali. 25Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake? 26Tsono ngati simungathe kuchita ngakhale kanthu kakang'ono kotere, bwanji mukudera nkhaŵa zinazo? 27#1Maf. 10.4-7; 2Mbi. 9.3-6Onani maluŵa m'mene amakulira. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu ai. Komatu kunena zoona, ngakhale mfumu Solomoni yemwe, mu ulemerero wake wonse, sankavala zokongola kulingana ndi limodzi lomwe mwa maluŵa ameneŵa. 28Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu? 29Nchifukwa chake musamadera nkhaŵa ndi kufunafuna zoti mudye, kapena zoti mumwe. 30Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu a mitundu yonse yapansipano. Atate anu amadziŵa kuti mumazisoŵa zimenezi. 31Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.”
Za chuma cha Kumwamba
(Mt. 6.19-21)
32“Inu nkhosa zanga, ngakhale muli oŵerengeka, musaope, pakuti kudakomera Atate anu kuti akupatseni Ufumu wake. 33Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge. 34Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.”
Kutsanzira antchito okhala maso
35 #
Mt. 25.1-13
“Khalani okonzeka kutumikira, ndipo nyale zanu zikhale zoyaka. 36#Mk. 13.34-36Khalani ngati antchito amene akudikira mbuye wao wochokera ku phwando la ukwati, kuti pamene afike ndi kugogoda, iwo amtsekulire msanga. 37Ngodala antchito amene mbuye wao pofika, aŵapeza ali maso. Ndithu ndikunenetsa kuti adzadzikonzekera, nadzaŵakhazika podyera, ndipo adzabwera nkumaŵatumikira. 38Ngodala antchitowo mbuye waoyo akadzaŵapeza ali choncho pamene iye adzafike, ngakhale pakati pa usiku kapena kuli pafupi kucha.
39 #
Mt. 24.43, 44 “Koma kumbukirani kuti, mwini nyumba akadadziŵiratu nthaŵi yoti mbala ifika, sibwenzi atalola kuti ithyole nyumba yake. 40Choncho inunso khalani okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene simukuyembekeza.”
Za wantchito wokhulupirika ndi wina wosakhulupirika
(Mt. 24.45-51)
41Pamenepo Petro adati, “Ambuye, kodi fanizoli mukuphera ife tokha, kapena mukuuza onse?” 42Yesu adati, “Tsono kapitao wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adzamuike kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake? 43Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi. 44Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse.
45“Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera.’ Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, amuna ndi akazi, ndiponso kumadya, kumamwa ndi kuledzera. 46Tsono mbuye wake adzangoti mbwe mwadzidzidzi, pa tsiku limene iye sakumuyembekeza. Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu osakhulupirika.
47“Wantchito amene akudziŵa zimene mbuye wake amafuna, koma osakonzekera kuzichita, adzamkwapula kwambiri. 48Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.”
Za kugaŵikana kwa anthu chifukwa cha Yesu
(Mt. 10.34-36)
49“Ndidabwera kudzaponya moto pa dziko lapansi, ndipo ndikadakonda utayaka kale. 50#Mk. 10.38Koma ndiyenera kuyamba ndaloŵa m'masautso akulu, ndipo mtima wanga sukhazikika mpaka zitachitika. 51Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Iyai, kunena zoona, osati mtendere koma kugaŵikana. 52Kuyambira tsopano m'banja limodzi mudzakhala anthu asanu ogaŵikana, atatu adzakangana ndi aŵiri, ndipo aŵiri adzakangana ndi atatu. 53#Mik. 7.6Bambo adzakangana ndi mwana wake wamwamuna, mwana wamwamuna adzakangana ndi bambo wake. Mai adzakangana ndi mwana wake wamkazi, mwana wamkazi adzakangana ndi mai wake. Apongozi adzakangana ndi mkazi wa mwana wao, ndipo mkaziyo adzakangana ndi apongozi akewo.”
Za kuzindikira nyengo
(Mt. 16.2-3)
54Yesu adauzanso anthu onse aja kuti, “Mukaona mtambo ukukwera kuzambwe, pompo mumati, ‘Mvula ikubwera,’ ndipo imabweradi. 55Mphepo yakumwera ikamaomba, mumati, ‘Kutentha,’ ndipo kumatenthadi.#12.54, 55: Mukaona mtambo ukukwera…mumati, ‘Kutentha,’ ndipo kumatenthadi: Ku dziko la Palestina anthu akaona mitambo kuzambwe, ankadziŵa kuti mvula ibwera. Ikaomba mphepo yakumwera, ankadziŵa kuti kutentha. 56Inu anthu achiphamaso, mumatha kuzindikira maonekedwe a dziko lapansi ndi a kuthambo, koma bwanji simutha kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika masiku omwe ano?”
Za kuyanjana ndi mnzako wamlandu
(Mt. 5.25-26)
57“Bwanji simutsimikiza nokha zoyenera kuchita? 58Monga pamene ukupita ndi mnzako wamlandu kwa woweruza, uyesetse kukonza mlanduwo mukali pa njira, kuwopa kuti angakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msilikali, ndipo msilikaliyo angakakuponye m'ndende. 59Ndithu ndikunenetsa kuti sudzatulukamo mpaka utalipira zonse.”
Currently Selected:
Lk. 12: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi