Lk. 18

18
Fanizo la mai wamasiye ndi munthu woweruza
1Yesu adaŵaphera fanizo pofuna kuŵaphunzitsa kuti azipemphera nthaŵi zonse, osataya mtima. 2Adati, “M'mudzi mwina mudaali woweruza wina amene sankaopa Mulungu kapena kulabadako za munthu. 3M'mudzi momwemo mudaalinso mai wamasiye. Iyeyu ankabwera kwa woweruza uja kudzampempha kuti, ‘Mundiweruzireko mlandu umene uli pakati pa ine ndi mdani wanga.’ 4Kwa nthaŵi yaitali woweruza uja ankakana, koma pambuyo pake adaganiza kuti, ‘Ngakhale sindiwopa Mulungu kapena kusamala munthu, 5komabe chifukwa mai wamasiyeyu akundivuta, ndimuweruzira mlandu wake, kuwopa kuti angandilemetse nako kubwerabwera kwake.’ ”
6Tsono Ambuye adati, “Mwamvatu mau a woweruza wosalungama uja. 7#Mphu. 35.19Nanga Mulungu, angaleke kuŵaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku? Kodi adzangoŵalekerera? 8Iyai, kunena zoona adzaŵaweruzira mlandu wao msanga. Komabe Mwana wa Munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?”
Fanizo la Mfarisi ndi wokhometsa msonkho
9Yesu adaŵapheranso fanizo anthu ena amene ankadziyesa olungama nkumanyoza anzao. 10Adati, “Anthu aŵiri adaapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera. Wina anali Mfarisi, wina anali wokhometsa msonkho. 11Mfarisiyo adaimirira nayamba kupemphera motere mumtima mwake: ‘Mulungu, ndikukuyamikani kuti ine sindili monga anthu ena onse ai. Iwowo ndi anthu akuba, osalungama ndi adama. Sindilinso monga wokhometsa msonkho uyu ai. 12Ine ndimasala zakudya kaŵiri pa mlungu, ndipo ndimapereka chachikhumi pa zonse zimene ndimapata.’ 13#Man. 1.8Koma wokhometsa msonkho uja adaima kutali, osafuna nkuyang'ana kumwamba komwe. Ankangodzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumanena kuti, ‘Mulungu, mundichitire chifundo ine wochimwane.’ ”
14 # Mt. 23.12; Lk. 14.11 Yesu popitiriza mau adati, “Kunena zoona, wokhometsa msonkhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo wodzichepetsa, adzamkuza.”
Yesu adalitsa ana
(Mt. 19.13-15; Mk. 10.13-16)
15Anthu ena ankabwera ndi ana omwe kwa Yesu kuti aŵakhudze. Ophunzira ake poona zimenezi, ankaŵazazira. 16Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere. 17Ndithu ndikunenetsa kuti amene salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzaloŵamo.”
Za munthu wina wolemera
(Mt. 19.16-30; Mk. 10.17-31)
18Mkulu wina adafunsa Yesu kuti, “Aphunzitsi abwino, kodi ndizichita chiyani kuti ndikalandire moyo wosatha?” 19Yesu adamuyankha kuti, “Ukunditchuliranji wabwino? Wabwinotu ndi mmodzi yekha, Mulungu basi. 20#Eks. 20.14; Deut. 5.18; Eks. 20.13; Deut. 5.17; Eks. 20.15; Deut. 5.19; Eks. 20.16; Deut. 5.20; Eks. 20.12; Deut. 5.16 Malamulo ukuŵadziŵa: Usachite chigololo, usaphe, usabe, usachite umboni wonama, lemekeza atate ako ndi amai ako.” 21Munthu uja adati, “Zonsezi ndakhala ndikuzitsata kuyambira ndili mwana.” 22Pamene Yesu adamva zimenezi, adamuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” 23Koma pamene munthu uja adamva zimenezi, adavutika mu mtima, pakuti adaali wolemera kwambiri.
24Yesu adamuyang'ana, nanena kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu. 25Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” 26Anthu amene adamva zimenezi adafunsa kuti, “Tsono nanga angathe kupulumuka ndani?” 27Yesu adati, “Zimene zili zosatheka ndi anthu, zimatheka ndi Mulungu.”
28Pamenepo Petro adati, “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani.” 29Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wosiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena makolo, kapena ana chifukwa cha Ufumu wa Mulungu, 30ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka kutsogoloko adzalandira moyo wosatha.”
Yesu aneneratu kachitatu za kufa ndi kuuka kwake
(Mt. 20.17-19; Mk. 10.32-34)
31Yesu adatengera ophunzira ake pambali, naŵauza kuti, “Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu, ndipo zonse zidzachitika zimene aneneri adalemba zokhudza Mwana wa Munthu. 32Akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamnyazitsa, ndi kumthira malovu. 33Akamkwapula, nkumupha, koma mkucha wake Iye adzauka.” 34Ophunzira aja sadamvetse konse zimenezi. Tanthauzo la mau ameneŵa linali lobisika kwa iwo, nchifukwa chake sadamvetsetse zimene Yesu ankanenazo.
Yesu achiritsa munthu wakhungu
(Mt. 20.29-34; Mk. 10.46-52)
35Pamene Yesu ankayandikira ku Yeriko, munthu wina wakhungu adaakhala pamphepete pa mseu akupemphapempha kwa anthu. 36Atamva anthu ambirimbiri akupita mumseumo, adafunsa kuti, “Kodi kuli chiyani?” 37Adamuyankha kuti, “Kukupita Yesu wa ku Nazarete.” 38Apo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!” 39Anthu amene anali patsogolo adamzazira, adati, “Khala chete!” Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide, chitireni chifundo!” 40Yesu adaima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atafika pafupi, Yesu adamufunsa kuti, 41“Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Iye adati, “Ambuye, ndikufuna kuti ndizipenyanso.” 42Yesu adamuuza kuti, “Penya. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” 43Nthaŵi yomweyo adapenyanso nayamba kutsata Yesu, akuthokoza Mulungu. Anthu onse aja ataona zimenezi, adatamanda Mulungu.

S'ha seleccionat:

Lk. 18: BLY-DC

Subratllat

Comparteix

Copia

None

Vols que els teus subratllats es desin a tots els teus dispositius? Registra't o inicia sessió