Lk. 19

19
Za Yesu ndi Zakeyo
1Yesu adaloŵa m'Yeriko, ulendo wake wobzola mzindawo. 2Kudafika munthu wina, dzina lake Zakeyo. Iyeyo anali mkulu wa okhometsa msonkho, ndipo anali wolemera. 3Ankafunitsitsa kuwona Yesu kuti ngwotani. Koma pakuti Zakeyoyo anali wamfupi, adalephera kumuwona chifukwa cha kuchuluka kwa anthu. 4Tsono adathamangira kutsogolo, nakakwera mu mkuyu kuti amuwone, chifukwa Yesu ankayenera kudzera pamenepo. 5Ndiye pamene Yesu adafika pamalopo, adayang'ana m'mwamba, namuuza kuti, “Zakeyo, fulumira, tsika, chifukwa lero ndikuyenera kukakhala nao kunyumba kwako.” 6Pompo Zakeyo adafulumira, natsika, kenaka nkukamlandiradi Yesu mokondwa kwambiri.
7Poona zimenezi, anthu onse adayamba kung'ung'udza. Adati, “Wakakhala kunyumba kwa munthu wochimwa.” 8Koma Zakeyo adaimirira nauza Ambuye kuti, “Ambuye, ndithudi ndidzapereka hafu la chuma changa kwa amphaŵi. Ndipo ngati ndidalandira kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ndidzamubwezera kanai.” 9Apo Yesu adamuuza kuti, “Chipulumutso chafika m'banja lino lero, popeza kuti ameneyunso ndi mwana wa Abrahamu. 10#Mt. 18.11Pajatu Mwana wa Munthu adabwera kudzafunafuna ndi kudzapulumutsa amene adatayika.”
Fanizo la ndalama
(Mt. 25.14-30)
11Anthu ankamva zimene Yesu ankalankhula. Tsono adaŵaphera fanizo, popeza kuti anali pafupi ndi Yerusalemu, ndipo anthuwo ankaganiza kuti Mulungu akhazikitsa ufumu wake posachedwa. 12Adati, “Munthu wina, wa fuko lomveka, adapita ku dziko lakutali kukalandira ufumu kuti pambuyo pake abwerenso kwao. 13Adaitana khumi mwa antchito ake naŵapatsa ndalama zasiliva khumi, aliyense yakeyake. Adaŵauza kuti, ‘Bachita nazoni malonda mpaka nditabwera.’ 14Koma anthu ake ankadana naye, choncho m'mbuyo muno adatuma nthumwi kuti zipite ku dziko lomwelo nkukanena kuti, ‘Ife sitikufuna konse kuti munthu ameneyu akhale mfumu yathu.’
15“Komabe iye adalandira ufumu uja. Tsono atabwerera kwao, adaitanitsa antchito aja adaaŵapatsa ndalamaŵa kuti adziŵe zimene adapindula. 16Woyamba adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi khumi.’ 17Mbuye wake adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zochepa kwambiri, udzalamulira midzi khumi.’ 18Wachiŵiri adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi asanu.’ 19Iyenso mbuye wake adamuuza kuti, ‘Iwe udzalamulira midzi isanu.’ 20Koma wina adadza nati, ‘Ambuye, nayi ndalama yanu ija. Ndidaaimanga pa kansalu. 21Ndinkakuwopani, popeza kuti ndinu munthu wankhwidzi. Mumalonjerera zimene simudaikize, ndiponso mumakolola zimene simudabzale.’ 22Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa, ndikutsutsa ndi mau ako omwe. Kani unkadziŵa kuti ndine munthu wankhwidzi, amene ndimalonjerera zimene sindidaikize, ndipo ndimakolola zimene sindidabzale. 23Nanga bwanji osaiika ku banki ndalama yangayo, kuti ine pobwera ndiilandire pamodzi ndi chiwongoladzanja chake?’ 24Atatero adauza anthu amene anali pomwepo kuti, ‘Mlandeni ndalamayi muipereke kwa amene ali ndi ndalama makumi khumiyo.’
25“Iwo adamuyankha kuti, ‘Pepani, ambuye, ameneyu ali kale ndi ndalama makumi khumi.’ 26#Mt. 13.12; Mk. 4.25; Lk. 8.18Koma iye adati, ‘Ndikunenetsa kuti aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. 27#Mt. 25.14-30Koma adani angaŵa, aja ankakana kuti ndikhale mfumu yaoŵa, bwera nawoni kuno, muŵaphe ine ndikuwona.’ ”
Yesu aloŵa ndi ulemu mu Yerusalemu
(Mt. 21.1-11; Mk. 11.1-11; Yoh. 12.12-19)
28Yesu atanena zimenezi, adatsogolera ophunzira ake kupita ku Yerusalemu. 29Atafika pafupi ndi midzi ya Betefage ndi Betaniya, pafupi ndi phiri lotchedwa Phiri la Olivi, adatuma ophunzira aŵiri, 30naŵauza kuti, “Pitani m'mudzi mukuwonawo. Mukakangoloŵamo mukapeza mwanawabulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukammasule, nkubwera naye kuno. 31Wina akakakufunsani kuti, ‘Mukummasuliranji?’ Mukati, ‘Ambuye ali naye ntchito.’ ” 32Aŵiriwo adapita, nakapezadi monga momwe Yesu adaaŵauzira. 33Pamene ankamasula mwanawabuluyo, eniake adaŵafunsa kuti, “Mukummasuliranji mwanawabuluyu?” 34Iwo adati, “Ambuye ali naye ntchito.” 35Tsono adapita naye kwa Yesu, nayamba kuyala zovala zao pa buluyo, nakwezapo Yesu. 36Pamene Yesu ankapita, anthu adamchitira ulemu pakuyala zovala zao mu mseu.
37Pamene ankayandikira Yerusalemu, pa matsitso a Phiri la Olivi, gulu lonse la omutsatira aja lidayamba kukondwerera. Adakweza mau, natamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene iwo adaziwona. 38#Mas. 118.26Adati, “Ndi yodala Mfumu imene ilikudza m'dzina la Ambuye. Mtendere Kumwamba, ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.”
39Apo Afarisi ena amene adaali m'khamumo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, auzeni ophunzira anuŵa aleke zimenezi.” 40Iye adati, “Ndikutitu iwoŵa akangokhala chete, ifuula ndi miyalayi.”
Yesu alira chifukwa cha Yerusalemu
41Yesu atayandikira, nkuwona Yerusalemu, adalira chifukwa cha mzindawo. 42Adati, “Ha, iwenso ukadangodziŵa lero lino zinthu zopatsa mtendere! Koma ai, tsopano maso ako sangathe kuziwona. 43Nthaŵi idzakufikira pamene adani ako adzakuzinga ndi machemba, nadzakuzungulira, nkukutsekereza ponseponse. 44Adzakusakaziratu iweyo pamodzi ndi anthu ako onse. Sadzasiya mwa iwe mwala pamwamba pa unzake, chifukwa chakuti sudazindikire nthaŵi imene Mulungu adaati adzakupulumutse.”
Yesu ayeretsa Nyumba ya Mulungu
(Mt. 21.12-17; Mk. 11.15-19; Yoh. 2.13-22)
45Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa anthu amene ankachita malonda m'menemo. 46#Yes. 56.7; Yer. 7.11 Adaŵauza kuti, “Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzakhala nyumba yopemphereramo.’ Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”
47 # Lk. 21.37 Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu tsiku ndi tsiku. Akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndiponso akulu a Ayuda#19.47: Akulu a ansembe…a Ayuda: Magulu atatuŵa pamodzi (akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo, ndi akulu a Ayuda) ndiwo Bwalo Lalikulu la Ayuda (Sanhedrin). Onani Matanthauzo. ankafuna kumupha, 48koma adaasoŵa chochita, chifukwa anthu onse ankatengeka nawo mtima mau ake.

S'ha seleccionat:

Lk. 19: BLY-DC

Subratllat

Comparteix

Copia

None

Vols que els teus subratllats es desin a tots els teus dispositius? Registra't o inicia sessió