YOHANE 5
5
Yesu achiritsa wopuwala kuthamanda la Betesida
1 #
Yoh. 2.13
Zitapita izi panali chikondwerero cha Ayuda; ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.
2 #
Neh. 3.1
Koma pali thamanda mu Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa mu Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu. 3M'menemo munagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, opunduka miyendo, opuwala.#5.3 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 4 Nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira pa thamandalo navundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachiritsidwa nthenda iliyonse imene anali nayo. 5Koma panali munthu wina apo, ali m'kudwala kwake zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu. 6Yesu, pakuona ameneyo alikugona, ndipo anadziwa kuti anatero nthawi yaikulu pamenepo, ananena naye, Ufuna kuchiritsidwa kodi? 7Wodwalayo anayankha, Ambuye, ndilibe wondiviika ine m'thamanda, paliponse madzi avundulidwa; koma m'mene ndilinkudza ine, wina atsika ndisanatsike ine. 8#Mat. 9.6; Mrk. 2.11; Luk. 5.24Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende. 9#Yoh. 9.14Ndipo pomwepo munthuyu anachira, nayalula mphasa yake, nayenda. Koma tsiku lomwelo linali la Sabata. 10#Eks. 20.10; Mat. 12.2; Mrk. 2.24Chifukwa chake Ayuda ananena kwa wochiritsidwayo, Ndi Sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako. 11Koma iyeyu anayankha iwo, Iye amene anandichiritsa, yemweyu anati kwa ine, Yalula mphasa yako, nuyende. 12Anamfunsa, Munthuyo ndani wonena ndi iwe, Yalula mphasa yako, nuyende? 13Koma wochiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani; pakuti Yesu anachoka kachetechete, popeza panali anthu aunyinji m'malo muja. 14#Mat. 12.45; Yoh. 8.11Zitapita izi Yesu anampeza mu Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa. 15Munthuyo anachoka, nauza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adamchiritsa.
Yesu adziwulula kuti ali Mwana wa Mulungu
16 #
Yoh. 1.15, 19, 27, 32 Ndipo chifukwa cha ichi Ayuda analondalonda Yesu, popeza anachita izo tsiku la Sabata. 17Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito. 18#Afi. 2Chifukwa cha ichi Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si chifukwa cha kuswa tsiku la Sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.
19 #
Yoh. 5.30; Yoh. 12.49 Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu ndinena kwa inu, sangathe Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo. 20#Mat. 3.17Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azichita yekha: ndipo adzamuonetsa ntchito zoposa izi, kuti mukazizwe. 21#Luk. 7.14-15; 8.54-55Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna. 22#Mat. 11.27Pakuti Atate saweruza munthu aliyense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana; 23#1Yoh. 2.23kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma Iye. 24#Yoh. 3.16, 18; 1Yoh. 3.14Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo. 25#Yoh. 5.28Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo. 26Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa Iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa Iye yekha; 27#Yoh. 5.22ndipo anampatsa Iye mphamvu ya kuchita mlandu, pakuti ali Mwana wa Munthu. 28#Yoh. 5.25; 1Ako. 15.52Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ake, 29#Mat. 25.32-33, 46nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.
30 #
Yoh. 5.19; 4.34 Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine. 31Ngati ndichita umboni wa Ine ndekha, umboni wanga suli woona. 32#Mat. 3.17Wochita umboni wa Ine ndi wina; ndipo ndidziwa kuti umboni umene Iye andichitire Ine uli woona. 33#Yoh. 1.15, 19, 27, 32Inu munatuma kwa Yohane, ndipo iye anachitira umboni choonadi. 34Ndipo Ine sindilandira umboni kwa munthu: koma ndinena izi, kuti inu mukapulumutsidwe. 35Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwake kanthawi. 36#Yoh. 10.25Koma Ine ndili nao umboni woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa ndizitsirize, ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate anandituma Ine. 37#Mat. 17.5Ndipo Atate wonditumayo, Iyeyu wandichitira Ine umboni. Simunamva mau ake konse, kapena maonekedwe ake simunaone. 38Ndipo mulibe mau ake okhala mwa inu; chifukwa kuti amene Iyeyu anatuma, inu simumkhulupirira ameneyo. 39#Luk. 24.27; Yoh. 5.46Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo; 40#Yoh. 1.11; 3.19ndipo simufuna kudza kwa Ine, kuti mukhale nao moyo. 41#Yoh. 5.34Ulemu sindiulandira kwa anthu. 42Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu mwa inu nokha. 43Ndadza Ine m'dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira Ine; akadza wina m'dzina lake la iye mwini, iyeyu mudzamlandira. 44#Yoh. 12.43; Aro. 2.29Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna? 45#Aro. 2.12Musayesa kuti Ine ndidzakunenezani inu kwa Atate; pali wakukunenezani, ndiye Mose, amene inu mumtama. 46#Gen. 3.15; 49.10; Mac. 26.22Pakuti mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira Ine; pakuti iyeyu analembera za Ine. 47Koma ngati simukhulupirira malembo a iyeyu, mudzakhulupirira bwanji mau anga?
Trenutno odabrano:
YOHANE 5: BLP-2018
Istaknuto
Podijeli
Kopiraj
Želiš li svoje istaknute stihove spremiti na sve svoje uređaje? Prijavi se ili registriraj
Bible Society of Malawi