1
YOHANE 6:35
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.
比較
YOHANE 6:35で検索
2
YOHANE 6:63
Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.
YOHANE 6:63で検索
3
YOHANE 6:27
Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.
YOHANE 6:27で検索
4
YOHANE 6:40
Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.
YOHANE 6:40で検索
5
YOHANE 6:29
Yesu anayankha nati kwa iwo, Ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo anamtuma.
YOHANE 6:29で検索
6
YOHANE 6:37
Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.
YOHANE 6:37で検索
7
YOHANE 6:68
Simoni Petro anamyankha Iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha.
YOHANE 6:68で検索
8
YOHANE 6:51
Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.
YOHANE 6:51で検索
9
YOHANE 6:44
Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.
YOHANE 6:44で検索
10
YOHANE 6:33
Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.
YOHANE 6:33で検索
11
YOHANE 6:48
Ine ndine mkate wamoyo.
YOHANE 6:48で検索
12
YOHANE 6:11-12
Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna. Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.
YOHANE 6:11-12で検索
13
YOHANE 6:19-20
Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anachita mantha. Koma Iye ananena nao, Ndine; musaope.
YOHANE 6:19-20で検索
ホーム
聖書
読書プラン
ビデオ