Logo YouVersion
Ikona Hľadať

Gen. 4

4
Kaini ndi Abele
1Adamu adakhala ndi mkazi wake Heva ndipo mkaziyo adatenga pathupi. Tsono adabala mwana wamwamuna, ndipo adati, “Ndalandira mwana wamwamuna mwa chithandizo cha Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Kaini. 2Pambuyo pake adabalanso Abele, mng'ono wa Kaini. Abele anali woŵeta nkhosa, koma Kaini anali mlimi. 3Patapita nthaŵi, Kaini adatenga zipatso zina zakumunda, nazipereka kwa Chauta. 4#Ahe. 11.4 Abele nayenso adatenga ana oyamba kubadwa a nkhosa zake, naŵapereka ngati nsembe, pamodzi ndi mafuta ake omwe. Tsono Chauta adakondwera ndi Abele, nalandira nsembe yake. 5Koma Kaini Chauta sadakondwere naye ndipo sadalandire chopereka chake. Chifukwa cha zimenezi, Kainiyo adakwiya kwambiri, kotero kuti nkhope yake inali yakugwa ndi yamasinya. 6Apo Chauta adafunsa Kainiyo kuti, “Kodi wakwiyiranji chotere? Chifukwa chiyani nkhope yako yagwa? 7Ukadachita zabwino, ndikadakondwera nawe. Koma chifukwa choti wachita zoipa, tchimo lakukhalirira pa khomo ngati chilombo cholusa. Likulakalaka kuti likugwire, koma iweyo uligonjetse tchimolo.”
8 # Lun. 10.3; Mt. 23.35; Lk. 11.51; 1Yoh. 3.12 Tsiku lina Kaini adauza mng'ono wake Abele kuti, “Tiye tikayende.” Atangopita kwa okha, Kaini adaukira mng'ono wakeyo namupha. 9Tsono Chauta adafunsa Kainiyo kuti, “Kodi mng'ono wako Abele ali kuti?” Iye adayankha kuti, “Sindikudziŵa. Kodi ndi ntchito yanga kusamala mng'ono wangayo?” 10#Ahe. 12.24 Chauta adamufunsanso kuti, “Kodi wachita chiyani? Magazi a mng'ono wako akulira kwa Ine kuchokera m'nthaka. 11Tsopano watembereredwa, sudzailimanso nthaka yomwe yamwa magazi a mng'ono wako, amene waŵakhetsa ndi manja ako. 12Ukamalima mbeu, nthakayo sidzakubalira, ndipo udzakhala womangoyendayenda, wosoŵa pokhala penipeni pa dziko lapansi.” 13Kaini adauza Chauta kuti, “Chilango chimenechi nchopitirira mphamvu zanga. 14Tsopano mwandipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu. Ndidzakhala wothaŵathaŵa pa dziko lapansi, ndipo aliyense wondipeza adzandipha.” 15Koma Chauta adamuyankha kuti, “Iyai, aliyense wopha iwe Kaini adzalangidwa, ndipo Ineyo ndidzamulipsira kasanunkaŵiri.” Motero Chauta adaika chizindikiro pa Kaini kuchenjeza aliyense kuti asamuphe Kainiyo. 16Tsono Kaini adachoka pamaso pa Chauta nakakhala m'dziko lotchedwa Nodi, kuvuma kwa Edeni.
Zidzukulu za Kaini
17Kaini adakhala ndi mkazi wake, mkaziyo adatenga pathupi, nabala mwana dzina lake Enoki. Tsono Kaini adamanga mzinda, nautcha dzina la mwana wake Enoki. 18Enoki adabereka mwana namutcha Iradi. Iradi adabereka Mehuyaele. Mahuyaele adabereka Metusaele amene adabereka Lameki. 19Lameki adakwatira akazi aŵiri. Dzina la mkazi wake woyamba linali Ada, la mkazi wachiŵiri linali Zila. 20Ada adabala Yabala, ndipo iyeyu ndiye kholo la onse oŵeta zoŵeta ndi okhala m'mahema. 21Mbale wake anali Yubale, ndipo ndiye kholo la onse okhoza kuimba zeze ndi toliro. 22Zila adabala Tubala-Kaini. Iyeyu ndiye kholo la onse ogwira ntchito yosula mkuŵa ndi zitsulo. Mlongo wa Tubala-Kainiyo anali Naama.
23Tsono Lameki adauza akazi akewo kuti,
“Iwe Ada ndi iwe Zila, mverani mau anga.
Tcherani khutu mumve, inu akazi anga.
Ine ndapha munthu chifukwa anandipweteka.
Ndamuphadi mnyamatayo amene anandimenya.
24Ngati wopha Kaini amlipsira kasanunkaŵiri,
ndiye kuti wopha ine Lameki
adzamlipsira kokwanira 77.”
Za Seti ndi Enosi
25Adamu adakhalanso ndi Heva mkazi wake, ndipo adatenga pathupi nabala mwana. Tsono Hevayo adati, “Mulungu wandipatsa mwana woloŵa m'malo mwa Abele uja amene adaphedwa ndi Kaini.” Mwanayo adamutcha Seti. 26Seti adabereka mwana namutcha Enosi. Nthaŵi imeneyo anthu adayamba kutama dzina la Chauta mopemba.

Aktuálne označené:

Gen. 4: BLY-DC

Zvýraznenie

Zdieľať

Kopírovať

None

Chceš mať svoje zvýraznenia uložené vo všetkých zariadeniach? Zaregistruj sa alebo sa prihlás