LUKA 10
10
Yesu atuma ophunzira makumi asanu ndi awiri
1Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini. 2#Mat. 9.37-38; Yoh. 4.35; 2Ate. 3.1Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake. 3Mukani; taonani, Ine ndituma inu ngati anaankhosa pakati pa mimbulu. 4#2Maf. 4.29; Mat. 10.9-10Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalonjere munthu panjira. 5#Mat. 10.12Ndipo m'nyumba iliyonse mukalowamo muthange mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi. 6Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m'menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu. 7#Mat. 10.10-11Ndipo m'nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wantchito ayenera mphotho yake; musachokachoka m'nyumba. 8#Mat. 10.11Ndipo m'mudzi uliwonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zomwezi akupatsani; 9#Mat. 3.2; Luk. 9.2ndipo chiritsani odwala ali momwemo nimunene nao, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. Koma kumudzi uliwonse mukalowako, 10ndipo salandira inu, m'mene mwatuluka kumakwalala ake nenani, 11#Mat. 10.14Lingakhale fumbi lochokera kumudzi kwanu, lomamatika kumapazi athu, tilisansira pa inu; koma zindikirani ichi, kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira. 12#Mat. 10.15Ndinena ndi inu kuti tsiku lijalo ku Sodomu kudzapiririka kuposa mudzi umenewo. 13#Mat. 11.21Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika m'Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa. 14Koma ku Tiro ndi Sidoni kudzapiririka m'chiweruziro, koposa inu. 15#Mat. 11.23Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku dziko la akufa. 16#Mat. 10.40; 1Ate. 4.8Iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana Iye amene anandituma Ine.
17 #
Luk. 10.1
Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu. 18#Yoh. 12.31Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba. 19#Mrk. 16.18Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse. 20#Afi. 4.3Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa m'Mwamba.
21 #
Mat. 11.25
Nthawi yomweyo Iye anakondwera ndi Mzimu Woyera, nati, Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi wa dziko, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu. 22#Mat. 28.18; Yoh. 1.18Zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira Iye. 23#Mat. 13.16Ndipo m'mene anapotolokera kwa ophunzira ake, ali pa okha, anati, Odala masowo akuona zimene muona. 24#1Pet. 1.10Pakuti ndinena ndi inu kuti aneneri ndi mafumu ambiri anafuna kuona zimene inu muziona, koma sanazione; ndi kumva zimene mukumva, koma sanazimve.
Fanizo la Msamariya wachifundo
25 #
Mat. 19.16
Ndipo taonani, wachilamulo wina anaimirira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani? 26Ndipo anati kwa iye, M'chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji? 27#Deut. 6.5; Lev. 19.18Ndipo iye anayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini. 28Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo. 29Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani? 30Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m'manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa. 31Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali ina. 32Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuona, anapita mbali ina. 33Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo, 34nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira. 35Ndipo m'mawa mwake anatulutsa marupiya atheka awiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe. 36Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m'manja a achifwamba? 37Ndipo anati, Iye wakumchitira chifundo. Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita nuchite iwe momwemo.
Marita ndi Maria
38 #
Yoh. 11.1
Ndipo pakupita paulendo pao Iye analowa m'mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lake Marita anamlandira Iye kunyumba kwake. 39Ndipo anali ndi mbale wake wotchedwa Maria, ndiye wakukhala pa mapazi a Ambuye, namva mau ake. 40Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize. 41Koma Ambuye anayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nuvutika ndi zinthu zambiri; 42koma chisoweka chinthu chimodzi, pakuti Maria anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.
Zvasarudzwa nguva ino
LUKA 10: BLPB2014
Sarudza vhesi
Pakurirana nevamwe
Sarudza zvinyorwa izvi
Unoda kuti zviratidziro zvako zvichengetedzwe pamidziyo yako yose? Nyoresa kana kuti pinda
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: