AROMA 6
6
Khristu anatithyolera mphamvu ya zoipa
1 #
Aro. 3.8
Chifukwa chake tidzatani? Tidzakhalabe m'uchimo kodi, kuti chisomo chichuluke? 2#Aro. 6.11; Akol. 2.20Msatero ai. Ife amene tili akufa ku uchimo, tidzakhala bwanji chikhalire m'menemo? 3#Agal. 3.27Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake? 4#Aro. 8.11; Akol. 2.12Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano. 5#Afi. 3.10-11Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m'chifanizidwe cha imfa yake, koteronso tidzakhala m'chifanizidwe cha kuuka kwake; 6#Agal. 2.20podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo; 7pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuuchimo. 8#2Tim. 2.11Koma ngati ife tinafa ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi Iye; 9#Chiv. 1.18podziwa kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siichitanso ufumu pa Iye. 10#Aheb. 9.27-28Pakuti pakufa Iye, atafa ku uchimo kamodzi; ndipo pakukhala Iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu. 11#Aro. 6.2; Agal. 2.19-20Chotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.
12 #
Mas. 119.133
Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake: 13#Aro. 12.1; 1Pet. 2.24ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo. 14#Aro. 8.2Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a chisomo.
Ife ndife akapolo a Mulungu
15 #
1Ako. 9.21
Ndipo chiyani tsono? Tidzachimwa kodi chifukwa sitili a lamulo, koma a chisomo? Msatero ai. 16#Mat. 6.24Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo? 17#2Tim. 1.13Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene munaperekedweracho; 18#Agal. 5.1ndipo pamene munamasulidwa kuuchimo, munakhala akapolo a chilungamo. 19Ndilankhula manenedwe a anthu, chifukwa cha kufooka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a chonyansa ndi a kusaweruzika kuti zichite kusaweruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a chilungamo kuti zichite chiyeretso. 20#Yoh. 8.34Pakuti pamene inu munali akapolo a uchimo, munali osatumikira chilungamo. 21#Aro. 7.5Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano? Pakuti chimaliziro cha zinthu izi chili imfa. 22#Yoh. 8.32Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha. 23#Gen. 2.17; Yoh. 3.16; Aro. 5.12; 1Pet. 1.4Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Currently Selected:
AROMA 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi