1
LUKA 9:23
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo Iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
LUKA 9:24
Pakuti amene aliyense akafuna kupulumutsa moyo wake, iye adzautaya; koma amene aliyense akataya moyo wake chifukwa cha Ine, iye adzaupulumutsa uwu.
3
LUKA 9:62
Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang'ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.
4
LUKA 9:25
Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wake?
5
LUKA 9:26
Pakuti amene aliyense adzachita manyazi chifukwa cha Ine ndi mau anga, Mwana wa Munthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika ndi ulemerero wake ndi wa Atate, ndi wa angelo oyera.
6
LUKA 9:58
Ndipo Yesu anati kwa iye, Nkhandwe zili nazo nkhwimba, ndi mbalame za kumwamba zisa, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu.
7
LUKA 9:48
Amene aliyense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira Iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.
Pekutangira
Bhaibheri
Zvirongwa
Mavideo