YOHANE 2
2
Yesu asandutsa madzi vinyo ku Kana
1Ndipo tsiku lachitatu panali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amake wa Yesu anali komweko. 2Ndipo Yesu yemwe ndi ophunzira ake anaitanidwa kuukwatiwo. 3Ndipo pakutha vinyo, amake wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo. 4#Yoh. 7.6, 30; 19.26Yesu nanena naye, Mkazi, ndili ndi chiyani ndi inu? Nthawi yanga siinafike. 5Amake ananena kwa atumiki, Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani. 6#Mrk. 7.3Ndipo panali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu. 7Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, ndendende. 8Ndipo ananena nao, Tungani tsopano, mupite nao kwa mkulu wa phwando. Ndipo anapita nao. 9Koma pamene mkuluyo analawa madzi osanduka vinyowo, ndipo sanadziwe kumene anachokera (koma atumiki amene adatunga madzi anadziwa), mkuluyo anaitana mkwati, 10nanena naye, Munthu aliyense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino. 11#Yoh. 1.14Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita m'Kana wa m'Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye. 12Zitapita izi anatsikira ku Kapernao, Iye ndi amake, ndi abale ake, ndi ophunzira ake; nakhala komweko masiku owerengeka.
Yesu ayeretsa Kachisi poyamba paja
(Mat. 21.1-17)
13 #
Yoh. 11.55
Ndipo Paska wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu. 14#Mat. 21.12; Mrk. 11.15; Luk. 19.45Ndipo anapeza m'Kachisi iwo akugulitsa ng'ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama alikukhala pansi. 15Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anatulutsa onse m'Kachisimo, ndi nkhosa ndi ng'ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza magome; 16nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda. 17#Mas. 69.9Ophunzira ake anakumbukira kuti kunalembedwa, Changu cha pa nyumba yanu chandidya ine. 18#Mat. 12.38Chifukwa chake Ayuda anayankha nati kwa Iye, Mutionetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi? 19#Mat. 26.61; Mrk. 14.58Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani Kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa. 20Pamenepo Ayuda anati, Zaka makumi anai ndi zisanu ndi chimodzi analimkumanga Kachisiyu, kodi inu mudzamuutsa masiku atatu? 21Koma Iye analikunena za Kachisi wa thupi lake. 22#Luk. 24.7-8Chifukwa chake atauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira kuti ananena ichi; ndipo anakhulupirira cholemba, ndi mau amene Yesu ananena.
23Koma pamene anali m'Yerusalemu pa Paska pachikondwerero, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi. 24Koma Yesu sanakhulupirire iwo kuti akhale nao, chifukwa Iye anadziwa anthu onse, 25#Mat. 9.4; Mrk. 2.8; Mac. 1.24ndipo sanasowe wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.
Zvasarudzwa nguva ino
YOHANE 2: BLPB2014
Sarudza vhesi
Pakurirana nevamwe
Sarudza zvinyorwa izvi
Unoda kuti zviratidziro zvako zvichengetedzwe pamidziyo yako yose? Nyoresa kana kuti pinda
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi