1
GENESIS 7:1
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno.
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
GENESIS 7:24
Ndipo anapambana madzi pa dziko lapansi masiku zana kudza makumi asanu.
3
GENESIS 7:11
Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.
4
GENESIS 7:23
Ndipo zinaonongedwa zamoyo zonse zimene zinali pa dziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa pa dziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m'chingalawa.
5
GENESIS 7:12
Ndipo mvula inali pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku.
Pekutangira
Bhaibheri
Zvirongwa
Mavideo