1
LUKA 23:34
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere.
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
LUKA 23:43
Ndipo Iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine m'Paradaiso.
3
LUKA 23:42
Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukireni m'mene mulowa Ufumu wanu.
4
LUKA 23:46
Ndipo pamene Yesu anafuula ndi mau akulu, anati, Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake.
5
LUKA 23:33
Ndipo pamene anafika kumalo dzina lake Bade, anampachika Iye pamtanda pomwepo, ndi ochita zoipa omwe, mmodzi kudzanja lamanja ndi wina kulamanzere.
6
LUKA 23:44-45
Ndipo ora lake pamenepo linali ngati lachisanu ndi chimodzi. Ndipo panali mdima pa dziko lonse kufikira ora lachisanu ndi chinai, ndipo dzuwa linada. Ndipo nsalu yotchinga ya m'Kachisi inang'ambika pakati.
7
LUKA 23:47
Ndipo pamene kenturiyo anaona chinachitikacho, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama.
Pekutangira
Bhaibheri
Zvirongwa
Mavideo