1
LUKA 16:10
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Iye amene akhulupirika m'chaching'onong'ono alinso wokhulupirika m'chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m'chachikulu.
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
LUKA 16:13
Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.
3
LUKA 16:11-12
Chifukwa chake ngati simunakhala okhulupirika m'chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona? Ndipo ngati simunakhala okhulupirika ndi zake za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni?
4
LUKA 16:31
Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.
5
LUKA 16:18
Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo.
Pekutangira
Bhaibheri
Zvirongwa
Mavideo