1
LUKA 12:40
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Khalani okonzeka inunso; chifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa Munthu akudza.
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
LUKA 12:31
Komatu tafunafunani Ufumu wake, ndipo izi adzakuonjezerani.
3
LUKA 12:15
Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.
4
LUKA 12:34
Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.
5
LUKA 12:25
Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wake?
6
LUKA 12:22
Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala.
7
LUKA 12:7
komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.
8
LUKA 12:32
Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.
9
LUKA 12:24
Lingirirani makungubwi, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!
10
LUKA 12:29
Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya, ndi chimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima.
11
LUKA 12:28
Koma ngati Mulungu aveka kotere udzu wa kuthengo ukhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang'ono?
12
LUKA 12:2
Koma kulibe kanthu kovundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.
Pekutangira
Bhaibheri
Zvirongwa
Mavideo